Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Lemba la Hagai 2:7 limati: “Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi.” Panopa tikuona kukwaniritsidwa kwa mawu amenewa. Tsopano ku Malawi kuno kuli ofalitsa opitirira 93,000 amene akulalikira uthenga wabwino. Pemphero lathu ndi lakuti Yehova apitirize kutidalitsa pamene tikumutumikira m’chaka cha 2016.