Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda January 1
“Kodi aliyense akanakhala kuti amatsatira mfundo iyi, bwenzi zinthu zili bwanji m’dzikoli? [Werengani Aheberi 13:18, ndipo yembekezerani ayankhe.] Baibulo limanena kuti tiyenera kuchita zinthu zonse moona mtima. Magazini iyi ikufotokoza zimene tingachite kuti tipewe chinyengo cha mtundu uliwonse.”
Galamukani! January
“Ndikufuna ndikupatseni Galamukani! ya mwezi uno. [M’patseni magaziniyo.] Taonani funso limene lili patsamba 2 komanso mayankho ake. Kodi inuyo mungayankhe bwanji funso ili? [Yembekezerani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tizikhala osangalala.”