Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda May 1
“Mutakhala ndi mphamvu zothetsa mavuto, kodi ndi vuto liti lomwe mungathetse? [Yembekezerani ayankhe.] Baibulo limanena kuti posachedwapa Mulungu athetsa vuto limeneli komanso ena onse. [Werengani lemba logwirizana ndi zimene wayankhazo. Malemba ake ndi monga, Danieli 2:44; Miyambo 2:21, 22; Mateyu 7:21-23 kapena 2 Petulo 3:7.] Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza kuti Mulungu adzachita zimenezi posachedwapa. Yafotokozanso mmene adzachitire zimenezi.”
Galamukani! May
“Kodi mukuganiza kuti zingatheke kuti umphawi uthe komanso kuti aliyense akhale ndi nyumba yabwino? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani zimene Mulungu walonjeza pa nkhaniyi. [Werengani Yesaya 65:21-22.] Galamukani! iyi ikufotokoza mmene Mulungu adzachitire zimenezi komanso zimene tingachite kuti tidzakhalepo pa nthawiyi.”