Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec. 15
“Panyengo ino ya pachaka, anthu ambiri amaganizira za kubadwa kwa Yesu. Kodi munayamba mwaganizirapo zoti anakulira m’banja lotani? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Luka 2:51, 52.] Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikufotokoza maphunziro abwino omwe tingatolepo pankhani ya m’Baibulo ya mmene Yesu analeredwera.”
Galamukani! Dec. 8
“Anthu ena akuda nkhaŵa kuti dzikoli lawonongedwa moti silingakonzedwenso. Kodi inu mumaganiza kuti zinthu sizidzasintha? [Yembekezani ayankhe.] Cholinga cha Mlengi sichinali choti dzikoli lidzakhale dzala loti anthu sangakhalemo. [Ŵerengani Yesaya 45:18.] Magazini iyi ikulongosola mmene dzikoli lidzapulumutsidwire.”
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Anthu ambiri amalakalaka padziko pano patakhala mtendere. Kodi mukuganiza kuti nthaŵi ina tidzaona mawu aŵa atakwaniritsidwa? [Ŵerengani Salmo 46:9. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikufotokoza mmene zimenezi zidzakwaniritsidwire ndiponso chifukwa chomwe tingakhulupirire lonjezo la Mulungu lakuti padziko lapansi sipadzakhala nkhondo.”
Galamukani! Dec. 8
“Kodi mumaganiza kuti anthu adzakhala ndi moyo ngati uwu wofotokozedwa apa? [Ŵerengani Yesaya 14:7. Kenako yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ili ndi mfundo zabwino kwambiri zomwe tingapindule nazo pamene tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu.” Sonyezani nkhani yakuti “Kodi Mungalimbane Bwanji ndi Zilakolako Zoipa?”