Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec. 15
“Chaka chilichonse nyengo ngati ino, anthu ambiri amakumbukira kubadwa kwa Yesu. Kodi mumadziŵa kuti pali zinthu zofunika kwambiri zimene tingaphunzire pankhani ya m’Baibulo ya kubadwa kwa Yesu? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno pitani pa tsamba 5, ndipo ŵerengani 2 Timoteo 3:16.] Nsanja ya Olonda iyi ikutchula zina mwa zinthuzi zimene tingaphunzirepo.”
Galamukani! Dec. 8
“Achinyamata ena amaganiza kuti sangatengere kwambiri zochita za anzawo. Ena amati saona kuti zochita za anzawo zingakhudze mmene iwo amachitira zinthu, ndipo kuti anthu amangokokomeza chabe kuti munthu umakhudzidwa ndi zochita za ena. Kodi mumaganiza kuti anthu amakhudzidwa ndi zochita za ena? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Aroma 12:2.] Galamukani! iyi ili ndi nkhani imene kwenikweni aikonza kuti ithandize achinyamata kuona kuti zochita za anthu ena zingakhudze kwambiri mmene iwo amachitira zinthu.”
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Nthaŵi zambiri munthu akakhala kuti wokondedwa wake wamwalira kapena wadwala, amafunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu amalola zimenezi?’ Mwina munafunsapo funso ngati limeneli. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amawamvera chisoni anthu ovutika. [Ŵerengani Yesaya 63:9a.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake tingakhulupirire kuti Mulungu adzathetsa mavuto.”
Galamukani! Dec. 8
“Chifukwa choopa zigaŵenga, anthu ambiri akufunsa ngati n’kwabwino kuyenda pandege. Kodi izi zimakudetsani nkhaŵa? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limati mavuto amagwera aliyense. [Ŵerengani Mlaliki 9:11.] Komabe, Galamukani! iyi ikufotokoza zimene mungachite mukakwera ndege kuti muzikhala wotetezeka kwambiri ndiponso kuti mtima wanu uzikhala uli m’malo.”