Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec. 15
“Panyengo ino yatchuthi, anthu ambiri amayesetsa kukhala achifundo ndi okoma mtima. Mukuganiza bwanji, kodi dziko silingakhale bwino anthu atamakhala okoma mtima chaka chonse? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani 1 Petulo 3:8.] Magazini iyi ikufotokoza ubwino wa kukoma mtima ndi mmene tingakusonyezere.”
Galamukani! Dec.
“Kodi mukuganiza kuti anthu amene tinkawakonda omwe anamwalira adzakhalanso ndi moyo? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limasonyeza kuti anthu amene anafa adzauka. [Werengani Salmo 68:20.] Magazini iyi ikufotokoza chimene sitiyenera kuopera imfa, chifukwa n’zotheka kudzakhalanso ndi moyo.”
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Anthu ambiri amapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Mwachitsanzo, taonani pemphero lotchuka lomwe Yesu anaphunzitsa otsatira ake. [Werengani Mateyo 6:9, 10.] Kodi munayamba mwaganizirapo kuti Ufumu umenewo n’chiyani ndi kuti udzabwera liti? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi.”
Galamukani! Jan.
“Kuyambira kalekale akazi akhala akusalidwa ndi kuchitiridwa nkhanza. Kodi mukuganiza kuti zimenezi zimachitika chifukwa chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mmene Baibulo limalangizira amuna za momwe ayenera kukhalira ndi akazi awo. [Werengani 1 Petulo 3:7.] Pogwiritsa ntchito Baibulo, magazini iyi ikusonyeza mmene Mulungu ndi Khristu amaonera akazi.”