Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Dec. 15
“Chaka chilichonse tikafika nthawi ino, anthu padziko lonse amakumbukira kubadwa kwa Yesu m’njira zosiyanasiyana. Kodi mukudziwa kuti zimene Baibulo linalosera zimasonyeza kuti kubadwa kwa Yesu kudzabweretsa mtendere wosatha? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Yesaya 9:6, 7.] Magazini iyi ikufotokoza mmene mtendere umenewo udzakhalire wotheka.”
Galamukani! Jan. 8
“Kodi mwaona kuti dzikoli likuika chidwi kwambiri pa kaonekedwe ka anthu? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mavuto ena amene amabwera chifukwa choganizira kwambiri za kukongola. Ikunenanso za kukongola kwina kumene kuli kofunika kwambiri.” Werengani 1 Petro 3:3, 4.
Nsanja ya Olonda Jan. 1
“Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti anthu ayenera kukonda anansi awo. [Werengani Mateyu 22:39.] Komano, mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani zipembedzo zimalowerera m’nkhondo zambiri ndi mikangano m’dzikoli? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ya Nsanja ya Olonda ikuyankha funso lakuti, Kodi chipembedzo chingagwirizanitse anthu?”
Galamukani! Jan. 8
“Kodi funso ili mungaliyankhe bwanji? [Werengani funso limene lili pachikutolo. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Zinthu zachilengedwe padziko lapansi lino zikutha mofulumira kwambiri. Komano, taonani lonjezo lodalirika ili. [Werengani Salmo 104:5.] Magazini iyi ya Galamukani! ikufotokoza mmene dzikoli lidzakhalirenso bwino posachedwapa.”