Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda Nov. 15
“Anthu ambiri amafuna kukhala ndi thanzi labwino ndiponso kukhala ndi moyo wautali. Koma ngati zikanakhala zotheka, kodi mukanakonda kukhala ndi moyo wosatha? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Yohane 17:3.] Magazini iyi ikunena za lonjezo la Baibulo la moyo wosatha. Ikufotokozanso mmene moyo udzakhalire lonjezo limeneli likadzakwaniritsidwa.”
Galamukani! Dec. 8
“M’zaka 20 zapitazi, pakhala kupita patsogolo kwambiri pa ntchito yothandiza kumvetsetsa za Edzi ndiponso kupereka chithandizo kwa odwala matendawa. Komabe anthu ambiri adakauzidwabe zabodza. [M’sonyezeni bokosi lakuti “Mfundo Zopeka Zonena za Edzi,” ndiyeno m’loleni aperekepo ndemanga.] Magazini iyi ikufotokoza mmene makolo angatetezere ana awo.” Ŵerengani Deuteronomo 6:6, 7.
Nsanja ya Olonda Dec. 1
Chinthu chimodzi chimene chimasiyanitsa anthu ndi zinyama ndicho nzeru zodziŵa chabwino ndi choipa. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amachita zinthu zoipa. Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani zili choncho? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Yeremiya 17:9 kapena Chivumbulutso 12:9.] Magazini iyi ikufotokoza zimene zingatithandize kuti tidziŵe ndi kuchita zimene zili zabwino.”
Galamukani! Dec. 8
“Munthu amafunikira kwambiri mabwenzi, ndipo kupita patsogolo kwa sayansi sikunasinthe zimenezi. Koma kodi mwaona masiku ano kuti zikuvuta kupeza mabwenzi apamtima chifukwa cha kusintha kwa zinthu? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Miyambo 18:24.] Magazini iyi ikufotokoza mmene tingapezere mabwenzi enieni ndi kukhala nawobe.”