Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/05 tsamba 4
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 11/05 tsamba 4

Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda Nov. 15

“Anthu ambiri amadabwa kuona kuti mavuto amene anthu akukumana nawo akuwonjezereka, m’malo mochepa. Kodi munayamba mwaganizirapo ngati zimene lemba ili likunena zingakhale chifukwa chake mavuto akuwonjezereka? [Werengani Chivumbulutso 12:9. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza njira zimene Mdyerekezi amasocheretsera anthu ndi zimene tingachite kuti tisanyengedwe nazo.”

Galamukani! Dec. 8

“Pafupifupi anthu 800 miliyoni akusowa chakudya, ngakhale kuti pakulimidwa chakudya chokwanira kudyetsa munthu wina aliyense padziko lapansi. Kodi zimenezo si zomvetsa chisoni? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikunena za vuto limene likukula lopezera chakudya anthu m’mizinda. Ikufotokozanso za lonjezo la m’Baibulo lonena za dziko lopanda njala.” Werengani Salmo 72:16a.

Nsanja ya Olonda Dec. 1

“Anthu akamva za liwu lakuti ‘Armagedo,’ ambiri amaganiza za kuwonongeka koopsa kwa anthu ambirimbiri. [Onetsani bokosi limene lili patsamba 3.] Kodi zingakudabwitseni kudziwa kuti Armagedo kwenikweni ndi chinthu chabwino kwambiri chimene chingatichitikire? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake.” Werengani 2 Petro 3:13.

Galamukani! Dec. 8

“Ndimaganiza zokuuzani za nthawi imene munthu aliyense adzakhala ndi malo abwino okhala. Kodi si zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri alibe nyumba zogona? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Yesaya 65:21, 22.] Magazini iyi ikufotokoza zifukwa zimene anthu akusowera nyumba. Ikufotokozanso za mmene Mulungu adzakwaniritsira lonjezo limene tawerengali.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena