Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Nov. 1
“Kodi mukuganiza kuti banja lingalimbe ngati mwamuna ndi mkazi wake akutsatira mfundo iyi ya m’Baibulo? [Werengani Yobu 31:1. Kenako yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize mwamuna ndi mkazi wake kukhalabe okhulupirika m’banja.” Sonyezani nkhani imene yayambira patsamba 18.
Galamukani Nov.
“Anthu ambiri akuvomereza kuti zinthu zachilengedwe m’nyanja zikutha mofulumira. Kodi mukuganiza kuti maboma a anthu angathetse vuto limeneli? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Mateyo 6:10.] Nkhani iyi ikufotokoza zifukwa zina zimene anthu akudera nkhawa ndiponso ikusonyeza mmene Mulungu adzathetsere vutoli.” Sonyezani nkhani imene yayambira patsamba 20.
Nsanja ya Olonda Dec. 1
“Nthawi ino, anthu ambiri akuganizira za Yesu. Ndiye tandiuzani, kodi Yesu wakhudza bwanji moyo wanu? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatilimbikitsa kutsatira chitsanzo cha Yesu. [Werengani 1 Petulo 2:21.] Kuchita zimenezi kungatithandize kukhala munthu wabwino ndiponso wosangalala. Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake.”
Galamukani Dec.
“Kwa zaka zambiri, anthu akhala akuganizira za funso ili. [Sonyezani funso limene lili pachikuto.] Kodi mukuganiza ndikuti kumene tingapeze yankho lomveka? [Yembekezani ayankhe.] Onani chifukwa chimene tingayembekezere Mulungu kuyankha funsoli. [Werengani Salmo 100:3.] Magazini iyi ikusonyeza zimene Baibulo limanena pankhaniyi.”