Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/07 tsamba 4
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 11/07 tsamba 4

Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda Nov. 15

“Tonsefe timafuna kukhala ndi moyo wabwino ndiponso osangalala. Pa lemba ili Yesu anatchula zimene zingatithandize kukhala osangalala, kodi mukugwirizana nazo? [Werengani Mateyo 5:3. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza kuti kukwaniritsa chibadwa chathu chofuna kulambira Mulungu, n’kumene kumapangitsa moyo wathu kukhala wabwino kwambiri.”

Galamukani! Nov.

“Masiku ano pamene sayansi yapita patsogolo, ndiponso anthu akungokayikira zilizonse, ambiri amaganiza kuti Baibulo n’lachikale. Kodi inu maganizo anu n’ngotani? [Yembekezani ayankhe.] Kodi mukudziwa kuti mawu alionse a m’Baibulo amene amanena za sayansi ndi olondola? [Werengani Yobu 26:7.] Galamukani! yapadera iyi ili ndi zifukwa zomveka bwino zokhulupirira Baibulo.”

Nsanja ya Olonda Dec. 1

“Kodi funso ili mungaliyankhe bwanji? [Werengani funso limene lili pa chikuto. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Cholinga cha Mulungu n’chakuti anthu onse akhale ogwirizana. [Werengani Salmo 46:8, 9.] Magazini iyi ili ndi nkhani ya m’Baibulo yofotokoza mmene anthu adzakhalire ogwirizana.”

Galamukani! Dec.

“Ena amaganiza kuti imfa ndi njira yopitira ku moyo wina, pamene ena amati ndi mathero a zonse. Kodi inuyo mumaganiza kuti tiyenera kuopa imfa? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yobu ananena poganizira imfa yake. [Werengani Yobu 14:14, 15.] Magazini iyi ikufotokoza bwino mfundo za m’Baibulo zosonyeza zimene zimachitika tikamwalira.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena