Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Nov.15
“Poona kuti chinyengo n’chofala padziko lapansi, anthu ena amanena kuti, ‘N’kuvutikiranji kuchita zinthu zabwino?’ Kodi nanunso munayamba mwaganizapo choncho? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mawu olimbikitsa awa. [Werengani Miyambo 2:21, 22.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chachikulu kwambiri chokhalira anthu achilungamo.”
Galamukani! Nov.
“Ena amaganiza kuti zinthu zonse zimene zimachitika, amazichititsa ndi Mulungu. Kukachitika zinthu zoipa, amati pali chifukwa chimene Mulungu wachitira zimenezo. Kodi inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Yakobe 1:13.] Magazini iyi ikusonyeza kuchokera m’Baibulo chimene chimachititsa kuti anthu azivutika ndi zimene Mulungu akuchita kuti athetse kuvutika.”
Nsanja ya Olonda Dec. 1
Kodi mukudziwa kuti ulosi wa m’Baibulo uwu ukukwaniritsidwa masiku ano? [Werengani Mateyo 24:11. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza ziphunzitso zina zimene zafala kwambiri masiku ano. Ikusonyezanso zimene tingachite kuti tisasocheretsedwe ndi aphunzitsi onyenga.”
Galamukani! Dec.
“Kodi mungasankhe ndani ngati mutafunsidwa kuti mutchule munthu woposa anthu ena onse amene anakhalapo? [Yembekezani ayankhe.] Ambiri amasankha Yesu. Taonani zimene iye adzachitira dziko lapansi akadzakhala Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu. [Aonetseni chithunzi cha pamasamba 8 ndi 9, ndipo werengani lemba limodzi lomwe lasonyezedwapo.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Yesu adzakwaniritsire zimenezi ndi nthawi imene adzachite zimenezi.”