February 29–March 6
ESITERE 1-5
Nyimbo Na. 86 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Esitere Anapulumutsa Anthu a Mulungu”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo ya Esitere.]
Esitere 3:5-9—Hamani ankafuna kupha anthu onse a Mulungu (ia 131 ndime 18-19)
Esitere 4:11–17; 5:1-2—Chikhulupiriro cha Esitere chinali champhamvu moti sankaopa kuphedwa (ia 125 ndime 2; 134 ndime 24-26)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Esitere 2:15—Kodi Esitere anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa komanso wodziletsa? (w06 3/1 9 ndime 7)
Esitere 3:2-4—N’chifukwa chiyani Moredekai ankakana kugwadira Hamani? (ia 131 ndime 18)
Kodi ndaphunzira chiyani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: Esitere 1:1-15 (Osapitirira 4 min.)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Perekani kabuku kakuti Mverani Mulungu. Muuzeni zimene mudzakambirane mukadzabweranso.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza kuti mwakumananso ndi munthu amene analandira kabuku kakuti Mverani Mulungu ndipo kambiranani tsamba 2 ndi 3. Muuzeni nkhani imene mudzaphunzire pa ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza mukuphunzira ndi munthu yemwe analandira kabuku kakuti Mverani Mulungu. Gwiritsani ntchito tsamba 4 ndi 5 la kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. (km 7/12 2-3 ndime 4)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika pampingo: (10 min.)
Fotokozani Mmene Ndandanda Yatsopano ya Misonkhano Yakuthandizirani?: (5 min.) Nkhani yokambirana. Funsani omvera kuti afotokoze mmene ndandanda yatsopanoyi yawathandizira. Alimbikitseni kuti azikonzekera bwino misonkhanoyi kuti azipindula kwambiri.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 26 ndime 18-23, ndi bokosi tsa. 269 (30 min.)
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu wa Mawa (3 min.)
Nyimbo Na. 149 ndi Pemphero