CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 1-5
Esitere Anapulumutsa Anthu a Mulungu
Esitere anasonyeza chikhulupiriro komanso kulimba mtima poteteza anthu a Mulungu
Esitere akanatha kuphedwa chifukwa chopita kwa mfumu popanda kuitanidwa. Iye anali atatha masiku 30 osaitanidwa ndi mfumu
Mfumu Ahasiwero amene ankadziwikanso ndi dzina lakuti Sasta I, anali munthu wankhanza. Panthawi ina anatenga munthu n’kumudula pakati kuti likhale chenjezo kwa anthu ena. Komanso anachotsa Mfumukazi Vasiti pa udindo chifukwa choti sanamvere
Esitere anafunika kuulula kuti anali Myuda ndiponso kuuza Mfumu Ahasiwero kuti yapusitsidwa ndi munthu amene inkamudalira