CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 1-10
Tizilemekeza Yesu Kuti Tikhale Pamtendere ndi Yehova
Baibulo linaneneratu kuti anthu adzakana kukhulupirira Yehova ndi Yesu
Baibulo linaneneratu kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana sadzamvera ulamuliro wa Yesu koma adzakhazikitsa maulamuliro awo
Ulosiwu unakwaniritsidwa koyamba pa nthawi yomwe Yesu anali padzikoli ndipo ukukwaniritsidwa kwambiri masiku ano
Wamasalimo ananena kuti anthu amang’ung’udza za zinthu zopanda pake, kutanthauza kuti zolinga zawo n’zopanda phindu ndipo sizingakwaniritsidwe ngakhale pang’ono
Amene amalemekeza Mfumu imene Yehova anasankha adzapeza moyo
Anthu onse omwe amatsutsa Mfumu ya Ufumu wa Mulungu adzawonongedwa
Aliyense amene amalemekeza Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu akhoza kupeza mtendere ndiponso adzapulumuka