CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 52-59
“Umutulire Yehova Nkhawa Zako”
Davide anakumana ndi mayesero ambiri othetsa nzeru. Pamene Salimo 55 linkalembedwa, n’kuti atakumana ndi zinthu monga . . .
Kunyozedwa
Kuzunzidwa
Kudziimba Mlandu
Mavuto a M’banja
Kudwala
Kuukiridwa
Davide anakwanitsa kupirira mavuto ake ngakhale kuti mavutowo ankaoneka ngati amukulira. Iye analemba malangizo othandiza anthu omwe amaona kuti n’zovuta kupirira mayesero omwe akukumana nawo. Anati: “Umutulire Yehova nkhawa zako.”
Kodi tingagwiritse ntchito bwanji vesili masiku ano?
Tizipemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima tikakumana ndi vuto linalake komanso ngati tikuda nkhawa ndi zinazake
Tizifufuza malangizo opezeka m’Mawu a Yehova komanso omwe gulu lake limapereka
Tiziyesetsa kupeza mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize kuchepetsa mavuto omwe takumana nawo