September 5-11
SALIMO 119
Nyimbo Na. 48 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“‘Muzitsatira Chilamulo cha Yehova’”: (10 min.)
Sal. 119:1-8—Kutsatira chilamulo cha Mulungu n’kumene kumatichititsa kukhalabe osangalala (w05 4/15 10 ndime 3-4)
Sal. 119:33-40—Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tikhale olimba mtima tikamakumana ndi mavuto (w05 4/15 13 ndime 12)
Sal. 119:41-48—Kudziwa bwino Mawu a Mulungu kumatithandiza kuti tizilalikira molimba mtima (w05 4/15 13 ndime 13-14)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Sal. 119:71—Kodi kukumana ndi mavuto kuli ndi ubwino wotani? (w06 9/1 14 ndime 4)
Sal. 119:96—Kodi mawu akuti “zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire” akutanthauza chiyani? (w06 9/1 14 ndime 5)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 119:73-93
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Nkhani yokambirana. Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyi. Limbikitsani ofalitsa kuti alembe ulaliki wawowawo.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Tingatani Ngati Tapeza Mwana Pakhomo Lomwe Tikufuna Kulalikira?”: (5 min.) Nkhani.
Zofunika Pampingo: (10 min.) Ngati palibe, mukhodza kukambirana zimene tikuphunzira mu Buku Lapachaka (yb16 59-62)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) ia mutu 6 ndime 1-14.
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 13 ndi Pemphero