Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 September tsamba 2
  • Ngati Tapeza Mwana Pakhomo Lomwe Tikufuna Kulalikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ngati Tapeza Mwana Pakhomo Lomwe Tikufuna Kulalikira
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Kulemekezana M’banja
    Galamukani!—2024
  • Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kuti Ayenerere Kubatizidwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 September tsamba 2

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingatani Ngati Tapeza Mwana Pakhomo Lomwe Tikufuna Kulalikira?

Alongo awiri akulalikira mayi ndi mwana wake

Tikapeza mwana pakhomo lomwe tikufuna kulalikira, tingachite bwino kumuuza kuti akaitane makolo ake. Zimenezi zingasonyeze kuti timalemekeza udindo wa makolowo. (Miy. 6:20) Ngati mwanayo watiuza kuti tilowe m’nyumba, tiyenera kukana. Ndipo akatiuza kuti makolo ake achokapo, tingachite bwino kudzapitanso ulendo wina.

Tikapeza mwana wamkulu, mwina wa zaka 15 mpaka 19, tingachitenso bwino kupempha chilolezo kwa makolo ake. Ngati makolowo palibe, tingafunse mwanayo ngati makolo ake amamulola kusankha yekha zinthu zoti aziwerenga. Akatiuza kuti amamuloleza, tingamupatse magazini kapena chinthu china choti awerenge. Tikhozanso kumuuza kuti angapeze zinthu zambiri zoti aziwerenga pa webusaiti yathu ya jw.org.

Tikamapitanso kukacheza ndi mwana amene anasonyeza chidwi, tingachite bwino kumupempha kuti tikumane ndi makolo ake. Kuchita zimenezi, kungatipatse mwayi wofotokozera makolowo chifukwa chimene tabwerera kunyumba kwawo. Tingawauzenso kuti malangizo a m’Baibulo angathandize banja lawo kuti liziyenda bwino. (Sal. 119:86, 138) Tikamachita zinthu mwaulemu kwa makolo a ana amene tawapeza tikamalalikira, zingapangitse kuti makolowo akhale ndi chidwi chofuna kumvetsera uthenga wathu. Zimenezi zingatipatse mpata wolalikira uthenga wabwino kwa banja lonse.—1 Pet. 2:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena