CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 22-24
Kodi Muli ndi “Mtima Wodziwa” Yehova?
Yehova anayerekezera anthu ndi nkhuyu
Ayuda okhulupirika omwe anali ku Babulo anali ngati nkhuyu zabwino
Mfumu Zedekiya komanso Ayuda ena osakhulupirika amene ankachita zoipa anali ngati nkhuyu zoipa
Kodi tingatani kuti tikhale ndi “mtima wodziwa” Yehova?
Yehova angatipatse ‘mtima womudziwa’ ngati timaphunzira Mawu ake ndi kugwiritsa ntchito zimene timaphunzirazo
Tiyenera kudzifufuza moona mtima n’kusintha makhalidwe ndi zilakolako zoipa zomwe zingawononge ubwenzi wathu ndi Yehova