June 5-11
YEREMIYA 51-52
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Nthawi Zonse Mawu a Yehova Amakwaniritsidwa”: (10 min.)
Yer. 51:11, 28—Yehova ananeneratu za munthu amene adzagonjetse Babulo (it-2-E 360 ¶2-3)
Yer. 51:30—Yehova ananeneratu kuti Babulo adzawonongedwa (it-2-E 459 ¶4)
Yer. 51:37, 62—Yehova ananeneratu kuti Babulo adzakhala bwinja (it-1-E 237 ¶1)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Yer. 51:25—Kodi n’chifukwa chiyani Babulo akutchulidwa kuti ndi “phiri lowononga”? (it-2-E 444 ¶9)
Yer. 51:42—Kodi “nyanja” imene ‘idzasefukire ndi kumiza Babulo,’ ikuimira chiyani? (it-2-E 882 ¶3)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Yer. 51:1-11
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Kukambirana “Zitsanzo za Ulaliki.” Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo. Limbikitsani ofalitsa kuti azionetsa mwininyumba zimene zili pa webusaiti yathu ya jw.org/ny pa gawo lakuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Mumakhulupirira Kwambiri Zimene Yehova Analonjeza”: (15 min.) Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Limbikitsani onse kuti nthawi zonse azikambirana maulosi a m’Baibulo ndi Akhristu anzawo n’cholinga choti azilimbitsa chikhulupiriro chawo.—Aroma 1:11, 12.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 2 ¶1-12
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 49 ndi Pemphero