CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EZEKIELI 6-10
Kodi Mudzalembedwa Chizindikiro Choti Ndinu Woyenera Kupulumuka?
Masomphenya a Ezekieli anakwaniritsidwa koyamba pamene Yerusalemu anawonongedwa. Nanga kodi adzakwaniritsidwa bwanji m’tsogolomu?
Munthu wokhala ndi kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera akuimira Yesu Khristu
Amuna 6 okhala ndi zida zophwanyira akuimira gulu lankhondo lakumwamba lotsogoleredwa ndi Khristu
A khamu lalikulu adzalembedwa chizindikiro akadzaweruzidwa kuti ndi nkhosa pa chisautso chachikulu