July 31–August 6
EZEKIELI 24-27
Nyimbo Na. 81 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ulosi Wonena za Kuwonongedwa kwa Turo Umatithandiza Kuti Tizikhulupirira Kwambiri Mawu a Yehova”: (10 min.)
Ezek. 26:3, 4—Kutatsala zaka zoposa 250, Yehova ananeneratu kuti mzinda wa Turo udzawonongedwa (si 133 ¶4)
Ezek. 26:7-11—Ezekieli anatchula mfumu komanso mtundu wa anthu womwe udzayambirire kuukira mzinda wa Turo (ce 216 ¶3)
Ezek. 26:4, 12—Ezekieli ananeneratu kuti mpanda, fumbi komanso nyumba za mumzinda wa Turo zidzaponyedwa m’madzi (it-1 70)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Ezek. 24:6, 12—Kodi dzimbiri la mphika likuimira chiyani? (w07 7/1 14 ¶2)
Ezek. 24:16, 17—N’chifukwa chiyani Ezekieli sankafunika kusonyeza chisoni pamene mkazi wake anamwalira? (w88 9/15 21 ¶24)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Ezek. 25:1-11
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Kapepala kalikonse—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Kapepala kalikonse—Mufotokozereni za vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? (Koma musaonetse vidiyoyi).
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 23 ¶13-15—Muitanireni kumisonkhano.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kukhulupirira Mawu a Mulungu Kumatithandiza Kupirira Tikakumana ndi Mayesero: (15 min.) Nkhani yokambirana yochokera pa malemba monga Yesaya 33:24; 65:21, 22; Yohane 5:28, 29 ndi Chivumbulutso 21:4. Onetsani vidiyo yakuti Kuyamikira Madalitso Amene Ufumu Udzabweretse. Limbikitsani onse kuti azidziyerekezera ali m’dziko latsopano, makamaka pamene akumana ndi mayesero.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 4 ¶16-23, komanso tsamba 48
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 88 ndi Pemphero