November 20-26
MIKA 1-7
Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mika.]
Mika 6:6, 7—Nsembe zimene timapereka kwa Yehova zimakhala zopanda phindu ngati timalephera kuchitira anzathu zinthu zabwino (w08 5/15 6 ¶20)
Mika 6:8—Zimene Yehova amafuna kuti tizichita n’zoti tikhoza kukwanitsa (w12 11/1 22 ¶4-7)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mika 2:12—Kodi ulosi umenewu unakwaniritsidwa bwanji? (w07 11/1 15 ¶5)
Mika 7:7—N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mtima ‘wodikira’ Yehova? (w03 8/15 24 ¶20)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mika 4:1-10
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Sal. 83:18—Kuphunzitsa Choonadi—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Eks. 3:14—Kuphunzitsa Choonadi—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) bhs 132 ¶20-21.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zofunika Pampingo: (6 min.)
Yehova Amafuna Kuti Tikhale Opatsa (Miy. 3:27): (9 min.) Onetsani vidiyoyi.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 10 ¶8-11 komanso tsamba 103 ndi 105 (kumanzere)
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 132 ndi Pemphero