CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MIKA 1-7
Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizichita Chiyani?
Yehova amatidziwa bwino kwambiri ndipo sayembekezera kuti tizichita zomwe sitingathe. Iye amaona kuti kugwirizana ndi Akhristu anzathu n’kofunika kwambiri pa kulambira kwathu. Ngati tikufuna kuti Yehova azilandira nsembe zathu tiyenera kukonda abale athu komanso kuwalemekeza.