November 27–December 3
NAHUMU 1–HABAKUKU 3
Nyimbo Na. 154 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khalanibe Maso”: (10 min.)
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Nahumu.]
[Onetsani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Habakuku.]
Hab. 2:1-4—Kuti tidzapulumuke pa tsiku lachiweruzo la Yehova, tiyenera ‘kuyembekezerabe’ (w07 11/15 10 ¶3-5)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Nah. 1:8; 2:6—Kodi mzinda wa Nineve unawonongedwa bwanji? (w07 11/15 9 ¶2)
Hab. 3:17-19—Ngakhale tikumane ndi mavuto panopa kapena pa Aramagedo, kodi tiyenera kukhala otsimikiza za chiyani? (w07 11/15 10 ¶11)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Hab. 2:15–3:6
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) hf—Muuzeni zimene mudzakambirane ulendo wotsatira.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) hf—Sonyezani mmene tingapangire ulendo wobwereza pogwiritsa ntchito kabuku kamene munamupatsa kale.
Nkhani: (Osapitirira 6 min.) w16.03 23-25—Mutu: Kodi Mungathandize Bwanji Mpingo Wanu?
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Khalanibe Maso Pamene Zinthu Zasintha”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onetsani vidiyo yakuti Anakhalabe Olimba Mwauzimu Atasamukira Kudera Lina.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) kr mutu 10 ¶12-19 komanso tsamba 105 (kumanja) ndi 107
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.) Dziwitsani abale ndi alongo kuti m’mwezi wa December tidzagawira Galamukani! yomwe ili ndi nkhani yapachikuto yakuti “Kodi Zinthu Padzikoli Zafika Poipa Kwambiri?” Vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki ya mlungu wotsatira idzayamba kupezeka pa JW Library kuyambira pa 30 November. Limbikitsani ofalitsa kuti adzayesetse kugawira magaziniyi kwa anthu ambiri.
Nyimbo Na. 129 ndi Pemphero