MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mapeto a Dziko Loipali Ali Pafupi Kwambiri
Onerani vidiyo yakuti, Mapeto a Dziko Loipali Ali Pafupi Kwambiri, ndipo kenako kambiranani mafunso otsatirawa omwe ndi okhudza lemba la Mateyu 24:34.
Kodi “zinthu zonsezi” zomwe zatchulidwa palembali ndi chiyani?
Kodi lemba la Ekisodo 1:6 limatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la mawu akuti “m’badwo”?
Kodi Yesu ankanena za m’badwo uti kwenikweni?
Kodi ndi magulu awiri ati amene apanga “m’badwo uwu”?
Kodi mawu a Yesu akusonyeza bwanji kuti tikukhala m’nthawi yamapeto yeniyeni?