Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki KomansoMoyo Wathu Wachikhristu ya May 2018
MAY 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWUA MULUNGU | MALIKO 7-8
“Nyamula Mtengo Wako Wozunzikirapo,ndi Kunditsatira Mosalekeza”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 8:34
adzikane yekha: Kapena kuti “kupereka ufulu wake kwa wina.” Mawu amenewa akusonyeza kuti munthu ayenera kudzikana, kapena kuti kudzipereka kwa Mulungu kuti azilamulira moyo wake. Mawuwa anachokera ku mawu achigiriki omwe angamasuliridwenso kuti munthu “ayenera kudziuza kuti ayi,” zomwe ndi zomveka tikaganizira kuti munthu amayenera kukana kuchita zofuna zake kapena zomukomera. (2 Akor. 5:14, 15) Maliko anagwiritsanso ntchito mawu achigirikiwo pamene ankanena zomwe Petulo anachita pokana Yesu.—Maliko 14:30, 31, 72.
Kodi Mukuthamanga Motani mu Mpikisano Wokalandira Moyo?
14 Yesu anauza ophunzira ake komanso gulu la anthu amene anasonkhana kuti, “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha (kapena kuti ‘adziuze kuti ayi,’ Charles B. Williams) ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo, ndi kunditsatira mosalekeza.” (Maliko 8:34) Ngati tikufuna kutsatira Yesu, tiyenera kukhala okonzeka kumutsatira “mosalekeza,” osati chifukwa chofuna kupindulapo kenakake. Tikutero chifukwa kuchita zinthu mosaganiza bwino ngakhale kamodzi, kungawononge zonse zimene takhala tikuchita, mwinanso kuchititsa kuti tisadzapeze moyo wosatha. Pamatenga nthawi yaitali kuti munthu akhale wolimba mwauzimu. Koma kupanda kusamala, zonse zikhoza kuwonongeka m’kanthawi kochepa ngati titasiya kukhala maso.
MAY 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWUA MULUNGU | MALIKO 9-10
“Masomphenya Olimbitsa Chikhulupiriro”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira paMaliko 9:7
mawu: M’mabuku a uthenga wabwino pali malo atatu pomwe Baibulo limamufotokoza Yehova akulankhula mwachindunji ndi anthu, ndipo malo achiwiri ndi pa Maliko 9:7.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira paMaliko 10:17, 18
Mphunzitsi Wabwino: Zikuoneka kuti munthuyu anagwiritsa ntchito mawu akuti “Mphunzitsi Wabwino” mwamwambo chabe komanso pongofuna kusangalatsa Yesu. Izi zili choncho chifukwa atsogoleri achipembedzo a panthawiyo ndi omwe ankafuna kuti anthu aziwalemekeza mwa njira imeneyi. Ngakhale kuti anthu ankamutchula kuti “Mphunzitsi” kapena “Ambuye” (Yoh. 13:13) Yesu sankafuna kuti anthu azimulemekeza koma kuti ulemerero wonse uzipita kwa Atate wake.
Palibe wabwino, koma Mulungu yekha: Zimene Yesu ananenazi zikusonyeza kuti ankadziwa zoti Yehova ndi amene ali woyenerera kuuza anthu chimene chili chabwino kapena choipa. Pamene Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Mulungu n’kudya chipatso cha mumtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa, anakhala ngati alanda udindo wa Mulungu wonena kuti ichi ndi chabwino kapena choipa. Mosiyana ndi anthu amenewa, Yesu anachita zinthu modzichepetsa kwambiri ndipo anasiyira udindo umenewu Atate wake. Yehova amatidziwitsa zimene zili zabwino komanso zoyenera kudzera m’Mawu ake.—Maliko 10:19.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Chimene Mulungu WachimangaPamodzi . . . ”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira paMaliko 10:4, 11
kalata yothetsa ukwati: Chilamulo chinkanena kuti munthu amene akufuna kuthetsa ukwati wake ayenera kuganizira mofatsa nkhaniyi pomuuza kuti alembe kalata yothetsera ukwati komanso kukumana ndi akulu kuti amuthandize maganizo. Cholinga cha Chilamulo chinali kuchepetsa mchitidwe womangothetsa maukwati mwachisawawa komanso chinkateteza akazi kuti asamaponderezedwe. (Deut. 24:1) Koma m’nthawi ya Yesu, atsogoleri achipembedzo anachititsa kuti kuthetsa ukwati kuzikhala kophweka. Katswiri wina wa mbiri yakale dzina lake Josephus, yemwe anali Mfarisi amene anathetsa banja lake, analemba kuti zinali zotheka “kuthetsa ukwati pa chifukwa chilichonse (ndipo zambiri mwa zifukwa zimene amuna ankathetsera ukwatizi, iwonso ankazichita).
wosiya mkazi wake: Kapena kuti “kuthamangitsa mkazi wake.” Mawu a Yesu omwe Maliko analembawa ndi ofanana ndi amene ali pa Mateyu 19:9 pomwe palinso chiganizo chakuti, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama. Zimene Maliko analembazi zikusonyeza kuti munthu sankaloledwa kuthetsa ukwati pokhapokha ngati wina m’banja wachita chigololo (por·neiʹa m’chigiriki).
wachita chigololo molakwira mkaziyo: Apa Yesu ankatsutsa zimene Arabi ankaphunzitsa zomwe zinkaloleza amuna kusiya akazi awo “pa chifukwa chilichonse.” (Mat. 19:3, 9) Mfundo yakuti munthu akhoza kuchita chigololo molakwira mkazi wake inali yachilendo kwa Ayuda ambiri. Arabi ankaphunzitsa kuti mwamuna sangachite chigololo molakwira mkazi wake. Iwo ankati akazi okha ndi amene angachite zimenezi. Yesu anasonyeza kuti amalemekeza akazi pamene ananena mfundo yakuti mwamunanso akachita chigololo ndiye kuti walakwira mkazi wake.
MAY 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWUA MULUNGU | MALIKO 11-12
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira paMaliko 12:41, 42
moponyamo zopereka: Mabuku akale achiyuda amanena kuti zoponyamo zopereka zimenezi zinkakhala mitsuko yooneka ngati chitoliro ndipo nthawi zambiri zinkakhala ndi bowo laling’ono pamwamba pake. Anthu ankaponyamo ndalama zomwe zinkagwira ntchito zosiyanasiyana. Mawu achigiriki omwe anagwiritsidwa ntchito palembali amapezekanso pa Yohane 8:20, pomwe anawamasulira kuti “malo a zopereka.” Mawu amenewa ayenera akutanthauza malo omwe anali Bwalo la Akazi. (Onani sgd mutu 15.) Malinga ndi mabuku ena a Arabi, zoponyamo zopereka zokwanira 13 zinaikidwa m’malo osiyanasiyana m’bwalo limeneli. Anthu enanso amanena kuti kukachisi kunali malo a zopereka aakulu kwambiri komwe kunkakasungidwa ndalama zonse zochokera moponyamo zopereka muja.
timakobidi tiwiri tating’ono: Mawu ake enieni, “maleputoni awiri omwe ndi ofanana ndi kwadiransi imodzi.” “Leputoni” ndi mawu achigiriki omwe amatanthauza kanthu kakang’ono kwambiri. Maleputoni zinali ndalama zazing’ono kwambiri zomwe zinkapangidwa ndi mkuwa ndipo zinkagwiritsidwa ntchito ku Isiraeli. Mawu achigiriki akuti ko·dranʹtes (omwe m’Chilatini ndi quadrans) ankanena za ndalama zachiroma zopangidwa ndi mkuwa ndipo dinari imodzi inkakhala yofanana ndi makwadiransi 64. Palembali, Maliko ankanena za ndalama yachiromayi pofotokoza ndalama zomwe Ayuda ankakonda kugwiritsa ntchito.—Onani sgd mutu 18.
Yehova Amayamikira Tikamamutumikira ndi Mtima Wathu Wonse
16 Pa Nisani 11, Yesu anakhala nthawi yaitali ali kukachisi komwe ankakambirana ndi anthu omwe ankamufunsa za komwe anatenga ulamuliro wochitira zozizwitsa komanso kuyankha mafunso okhudza misonkho, kuukitsidwa kwa akufa ndi nkhani zina. Anadzudzulanso alembi ndi Afarisi pa nkhani zosiyanasiyana monga “kudyerera nyumba za akazi amasiye.” (Maliko 12:40) Kenako Yesu anakhala pansi ndipo n’kutheka kuti munali m’Bwalo la Akazi. Malinga ndi mwambo wachiyuda, m’bwaloli munali zoponyamo zopereka zokwanira 13. Iye ankayang’ana mwachidwi anthu amene ankapereka zopereka zawo. Panabwera anthu olemera ambiri ndipo ena ankapereka ndalama modzionetsera kuti ena awaone ngati anthu abwino. (Yerekezerani ndi Mateyu 6:2.) Yesu anachita chidwi kwambiri ndi mayi winawake. Anthu ena sakanaona zinthu zapadera zimene mayiyo anachita. Koma Yesu amene ankatha kuona mumtima, anadziwa kuti mayiyo anali “wamasiye.” Anadziwanso kuchuluka kwa ndalama zimene anapereka kuti tinali “timakobidi tiwiri tating’ono.”—Maliko 12:41, 42.
17 Yesu anaitana ophunzira ake kuti aone zimene mayiyo anachita chifukwa ankafuna kuwaphunzitsa phunziro lofunika kwambiri. Iye anawauza kuti, “mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa onse amene aponya ndalama moponya zoperekamo.” Mayiyo analidi atapereka “zonse zimene anali nazo.” Zimene anachitazi zinasonyeza kuti ankadalira kwambiri Yehova. Munthu amene anapereka mphatso yooneka ngati yosanunkha kanthuyi ndi amene Yesu ananena kuti tiyenera kutengera chitsanzo chake tikamafuna kupereka zinthu kwa Mulungu. Kwa Yehova, mphatso imene anaperekayi inali yamtengo wapatali.—Maliko 12:43, 44; Yak. 1:27.
Kodi Mumam’patsa Yehova Nsembe Zabwino Kwambiri?
Tingaphunzire zambiri kuchokera mu nkhani ya mayi wamasiye wosauka. Phunziro lalikulu ndi loti tonsefe tingathe kuthandiza nawo pa ntchito za Ufumu ndi chuma chathu. Komabe Yehova amayamikira tikamamupatsa zinthu zimene ifeyo timaona kuti n’zamtengo wapatali kwambiri. Ndiye kodi timapereka kwa Yehova zinthu zimene timaona kuti tilibe nazo ntchito, kapena timamupatsa nsembe zabwino kwambiri?
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira paMaliko 11:17
nyumba yopemphereramo mitundu yonse: Pa anthu atatu olemba mabuku a Uthenga Wabwino omwe anagwira mawu lemba la Yesaya 56:7, ndi Maliko yekha amene analemba mawu akuti “mitundu yonse.” (Mat. 21:13; Luka 19:46) Kachisi wa ku Yerusalemu anali malo omwe Aisiraeli komanso anthu oopa Mulungu amitundu ina, ankayenera kupita kuti azikalambira ndi kupemphera kwa Yehova. (1 Maf. 8:41-43) Mpake kuti Yesu anadzudzula Ayuda omwe anasandutsa kachisiyu kukhala malo amalonda komanso phanga la achifwamba. Zimene ankachitazi zinkapangitsa kuti anthu amitundu yonse azilephera kupita kunyumba ya Yehova yopemphereramo. Izi zinkachititsa kuti anthuwo alephere kumudziwa bwino Mulungu.
MAY 28–JUNE 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWUA MULUNGU | MALIKO 13-14
“Pewani Msampha Woopa Anthu”
it-2 619 ¶6
Petulo
Wophunzira wina, yemwenso ankatsatira Yesu popita ku nyumba ya mkulu wa ansembe, anathandiza Petulo kuti alowe m’bwalo lamkati. (Yoh. 18:15, 16) Petulo sanakhale pamalo obisika koma m’malo mwake anapita n’kumakawotha nawo moto. Kuwala kwa motowo kunachititsa kuti anthu amuzindikire kuti ankayenda ndi Yesu. Chinanso chimene chinam’gwiritsa ndi mmene ankalankhulira chifukwa ankachita kudziwika kuti ndi wa ku Galileya. Anthuwo atamufunsa, Petulo anakana maulendo atatu kuti sakumudziwa Yesu ndipo ankachita kulumbira. Tambala atalira kachiwiri, Yesu “anacheuka ndi kuyang’ana Petulo.” Nthawi yomweyo Petulo anatuluka panja ndi kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri. (Mat. 26:69-75; Maliko 14:66-72; Luka 22:54-62; Yoh. 18:17, 18) Komabe Mulungu anali atayankha pemphero limene Yesu anapempherera Petulo moti chikhulupiriro chake sichinathe.—Luka 22:31, 32.