Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya August 2018
AUGUST 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 17-18
“Muzisonyeza Kuyamikira”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 17:12, 14
amuna 10 akhate: Zikuoneka kuti kale, anthu akhate ankakonda kukhala komanso kuyendera limodzi ndipo ankathandizana. (2 Maf. 7:3-5) Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti anthu akhate azikhala kwaokha. Ngati munthu wakhate akudutsa pafupi ndi anthu ankafunika kuchenjeza anthuwo pofuula kuti: “Wodetsedwa, wodetsedwa!” (Lev. 13:45, 46) Mogwirizana ndi zimene Chilamulo chinkanena, akhatewa anaima patali ndi Yesu.
Pitani mukadzionetse kwa ansembe: Popeza Yesu ali padziko lapansi ankatsatira Chilamulo, ankalemekeza udindo wa ansembe moti anauza akhate amene anawachiritsa kuti apite kukadzionetsa kwa ansembewo. (Mat. 8:4; Maliko 1:44) Chilamulo chinkanena kuti wansembe ankayenera kutsimikizira ngati munthu amene anali ndi khate wachira. Kenako munthu amene anali ndi khateyo ankayenera kupita kukachisi atatenga mbalame zamoyo ziwiri zosadetsedwa, nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope kukapereka nsembe.—Lev. 14:2-32.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 17:10
opanda pake: Mawu ake enieni, “opanda ntchito, osafunika.” Fanizo la Yesuli silisonyeza kuti akapolo kapena kuti ophunzira ake, azidziona kuti ndi opanda ntchito kapena osafunika. Mawu akuti “opanda pake” amasonyeza kuti akapolowo ankayenera kukhala odzichepetsa, ndipo sankayembekezera kupatsidwa ulemu wapadera kapena kutamandidwa chifukwa cha zimene achita. Akatswiri ena amanena kuti mawu amene anagwiritsidwa ntchito pamenepa ndi okokomeza, otanthauza kuti “tangokhala akapolo chabe ndipo sitikuyenera kupatsidwa ulemu wapadera.”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 18:8
chikhulupiriro: Mawu akuti “chikhulupiriro” omwe Yesu ananena amatanthauza chikhulupiriro chapadera chofanana ndi chimene mayi wamasiye wa m’fanizo la Yesu anali nacho. (Luka 18:1-8) Zimenezi zikuphatikizapo kukhulupirira kuti Mulungu amayankha mapemphero komanso kuti adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa atumiki ake okhulupirika. Yesu sanayankhe funso lomwe lili muvesi 8, chifukwa iye ankafuna kuti ophunzira ake aone ngati chikhulupiriro chawo chinali champhamvu. Fanizo lonena za pemphero komanso chikhulupiriro linali lofunika kwambiri chifukwa Yesu anali atangomaliza kumene kufotokoza mayesero omwe ophunzira ake adzakumane nawo.—Luka 17:22-37.
AUGUST 13-19
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 19-20
“Zomwe Tikuphunzira M’fanizo la Ndalama 10 za Mina”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 19:43
adzamanga mpanda wazisonga kukuzungulira: Mawu achigiriki akuti khaʹrax amapezeka pavesi lokhali m’Malemba Achigiriki. Mawuwa amatanthauza “mitengo yosongoka kapena mitengo yomangira mpanda.” Amatanthauzanso “mpanda umene asilikali amamanga ndi mitengo.” Mawu a Yesuwa anakwaniritsidwa mu 70 C.E. pamene asilikali achiroma motsogoleredwa ndi Tito anamanga mpanda kuzungulira Yerusalemu. Cholinga cha Tito pomanga mpandawu chinali choti Ayuda asathawe mumzindawo, awakhaulitse kuti avomere kuti agonja komanso kuti chakudya mumzindawo chiwathere n’cholinga choti angodzipereka. Kuti apeze mitengo yomangira mpanda umenewu, asilikali achiroma anadula mitengo yomwe inali m’deralo.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 20:38
pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo: Kapena kuti “pamaso pa Yehova anthuwa amakhala ngati sanamwalire n’komwe.” Baibulo limasonyeza kuti anthu amoyo omwe samachita zimene Mulungu amafuna, iye amawaona ngati akufa. (Aef. 2:1; 1 Tim. 5:6) Mofanana ndi zimenezi, Yehova amaona kuti atumiki ake omwe anamwalira, adakali ndi moyo chifukwa iye wakonza zoti adzawaukitsa ndipo zimenezi sizingalephereke ngakhale pang’ono.—Aroma 4:16, 17.
AUGUST 20-26
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 21-22
“Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 21:33
Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka: Malemba ena amasonyeza kuti kumwamba komanso dziko lapansi zidzakhalapo mpaka kalekale. (Gen. 9:16; Sal. 104:5; Mlal. 1:4) Choncho mawu a Yesuwa angokhala okokomeza. Mawuwa akutanthauza kuti zinthu zomwe ndi zosatheka zitachitikadi, monga kuchoka kwa kumwamba ndi dziko lapansi, mawu a Yesu akhozabe kukwaniritsidwa. (Yerekezerani ndi Mat. 5:18.) Choncho kumwamba ndi dziko lapansi zimene zafotokozedwa palembali ndi zophiphiritsa ndipo pa Chivumbulutso 21:1, zinatchulidwa kuti “kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale.”
mawu anga sadzachoka ayi: Kapena kuti “Mawu angawa sadzalephereka ngakhale pang’ono.” Mawuwa m’Chigiriki amasonyeza kutsutsa mwamphamvu mfundo inayake, zomwe zikusonyeza kuti mawu a Yesuwa adzakwaniritsidwa ndithu.
AUGUST 27–SEPTEMBER 2
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 23-24
“Muzikhala Okonzeka Kukhululukira Ena”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 23:31
pamene mtengo uli wauwisi, . . . mtengowo ukadzauma: Zikuoneka kuti Yesu ankanena za mtundu wa Ayuda. Mtunduwu unali ngati mtengo womwe unali usanaferetu chifukwa Yesu anali adakali pakati pawo ndipo Ayuda ena ankamukhulupirira. Koma Yesu anali atatsala pang’ono kuphedwa ndipo Ayuda okhulupirika akanadzozedwa ndi mzimu woyera n’kukhala Isiraeli wauzimu. (Aroma 2:28, 29; Agal. 6:16) Pa nthawi imeneyo, mtengo uja womwe ukuimira mtundu weniweni wa Isiraeli ukanakhala utaumiratu.—Mat. 21:43.
nwtsty zithunzi ndi mavidiyo
Msomali M’fupa Lachidendene
Ichi ndi chithunzi chongoyerekezera chosonyeza msomali wautali masentimita 11.5 (mainchesi 4.5) utalowa mufupa lachidendene. Fupa lenileni linapezeka m’chaka cha 1968, pamene anthu ena ankafukula zinthu zakale chakumpoto kwa Yerusalemu ndipo zikuoneka kuti fupali ndi la m’nthawi ya Aroma. Fupa lokhala ndi msomali limeneli ndi umboni wakuti pa nthawiyo ankagwiritsa ntchito misomali akamapha anthu powakhomerera pamtengo. Msomaliwu uyenera ndi wofanana ndi umene asilikali achiroma anagwiritsa ntchito pokhomerera Yesu pamtengo. Fupali linapezeka m’bokosi linalake lamwala, lomwe munaikidwa mafupa a munthu wina amene anaphedwa. Zimenezi zikusonyeza kuti munthu akaphedwa mochita kukhomereredwa pamtengo ankaikidwanso m’manda.