MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Akhristu Oona Amadziwika Chifukwa cha Chikondi—Muzisangalala ndi Choonadi
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Potengera chitsanzo cha Yesu, tiyenera kumayesetsa kuchitira umboni choonadi chokhudza zolinga za Mulungu. (Yoh. 18:37) Tiyeneranso kumasangalala ndi choonadi, kulankhula zoona komanso kupitirizabe kuganizira zinthu zilizonse zoona ngakhale kuti tikukhala m’dziko limene anthu ambiri ndi achinyengo komanso opanda chilungamo.—1 Akor. 13:6; Afil. 4:8.
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
Tisamamvetsere kapena kufalitsa nkhani zamiseche.—1 Ates. 4:11
Tisamasangalale anthu ena akakumana ndi mavuto
Tizisangalala ndi zinthu zabwino komanso zolimbikitsa
ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIKONDANA’—MUZISANGALALA NDI CHOONADI, OSATI NDI ZOSALUNGAMA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi Debbie anasonyeza bwanji kuti ‘ankasangalala ndi zosalungama’?
Kodi Alice anasintha bwanji nkhani imene Debbie ankakamba n’kuyamba kukambirana zolimbikitsa?
Kodi ndi zinthu zina ziti zolimbikitsa zimene tingakambirane?
Muzisangalala ndi choonadi, osati ndi zosalungama