Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr18 November tsamba 1-4
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya November 2018

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya November 2018
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2018)
  • Timitu
  • NOVEMBER 5-11
  • Kufufuza Mfundo Zothandiza
  • NOVEMBER 12-18
  • Kufufuza Mfundo Zothandiza
  • NOVEMBER 19-25
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2018)
mwbr18 November tsamba 1-4

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya November 2018

NOVEMBER 5-11

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 20-21

“Kodi Umandikonda Ine Kuposa Izi?”

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 21:15, 17

Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: Zimene Yesu ankakambirana ndi Petulo zinachitika pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Petulo anamukana maulendo atatu. Yesu anamufunsa maulendo atatu kuti adziwe ngati ankamukonda kwambiri mpaka “Petulo anamva chisoni.” (Yoh. 21:17) Pa zimene Yohane analemba pa Yohane 21:15-17 anagwiritsa ntchito mawu awiri achigiriki, a·ga·paʹo, omwe palembali anawamasulira kuti kukonda ndi phi·leʹo, omwe anawamasulira kuti kukonda kwambiri. Kawiri konse Yesu anafunsa Petulo kuti “kodi umandikonda?” Maulendo onsewo Petulo anayankha motsimikiza kuti ‘amamukonda kwambiri.’ Pomaliza Yesu anafunsa Petulo kuti: “Kodi ine umandikonda kwambiri?” Ndipo iye anayankhanso kuti amamukonda kwambiri. Nthawi iliyonse imene Petulo anayankha kuti amamukonda, Yesu anatsindika mfundo yakuti chikondi chakecho chiyenera kumulimbikitsa kudyetsa komanso ‘kuweta’ mwauzimu ophunzira ake omwe anawatchula kuti nkhosa zake, kapena “ana a nkhosa.” (Yoh. 21:16, 17; 1 Pet. 5:1-3) Yesu analola kuti Petulo amutsimikizire maulendo atatu kuti amamukonda ndipo kenako anamupatsa udindo wosamalira nkhosa zake. Pochita zimenezi Yesu anasonyeza kuti anakhululukira ndi mtima wonse Petulo pomukana katatu.

kodi umandikonda ine kuposa izi?: Mawu akuti “kuposa izi” angakhale ndi matanthauzo angapo. Akatswiri ena amaona kuti tanthauzo labwino la funsoli ndi lakuti, “Kodi umandikonda ine kuposa mmene umakondera ophunzira enawa?” kapena “Kodi umandikonda ine kuposa mmene ophunzira enawa amandikondera?” Komabe tanthauzo lomwe likuoneka kuti ndi lolondola ndi lakuti “kodi umandikonda ine kuposa mmene umakondera zinthu izi?” kutanthauza nsomba zimene anagwira kapenanso zinthu zina zokhudzana ndi ntchito yosodza. Choncho mfundo yaikulu ya funsoli ndi yakuti: ‘Kodi umandikonda ine kuposa chuma kapena zinthu za m’dzikoli? Ngati umandikonda ine, dyetsa nkhosa zanga.’ Funsoli linali lomveka tikaganizira mbiri ya Petulo. Ngakhale kuti iye anali mmodzi mwa ophunzira oyambirira a Yesu (Yoh. 1:35-42), sankamutsatira nthawi zonse chifukwa nthawi zina ankabwerera ku ntchito yake yausodzi. Patapita miyezi ingapo, Yesu anauza Petulo kuti asiye ntchito ya usodzi wa nsomba n’kukhala ‘msodzi wa anthu.’ (Mat. 4:18-20; Luka 5:1-11) Komanso Yesu atangophedwa, Petulo ananena kuti akukapha nsomba ndipo atumwi ena anamutsatira. (Yoh. 21:2, 3) Choncho apa zikuoneka kuti Yesu ankakumbutsa Petulo kufunika kosankha chimodzi. Kodi iye akanaika patsogolo ntchito yake yausodzi yomwe ikuimiridwa ndi nsomba zomwe zinali patsogolo pawo, kapena akanaika patsogolo ntchito yodyetsa mwauzimu nkhosa kapena kuti otsatira a Yesu?—Yoh. 21:4-8.

kachitatu: Petulo anakana Yesu maulendo atatu ndipo Yesu anamupatsa mwayi woti atsimikizire kuti amamukonda maulendonso atatu. Petulo atachita zimenezo, Yesu anamuuza kuti ayenera kusonyeza chikondi chimenecho pomaona kuti zinthu zopatulika ndi zofunika kwambiri kuposa zina zonse. Petulo limodzi ndi amuna ena audindo ankayenera kudyetsa, kulimbikitsa komanso kuweta nkhosa zokhulupirika za Khristu. Nkhosazo zinali Akhristu odzozedwa, komabe iwo ankayenera kudyetsedwa mwauzimu.—Luka 22:32.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh 20:17

Usandikangamire: Mawu a m’Chigiriki akuti haʹpto·mai angatanthauze “kugwira” kapena “kukakamira.” Mabaibulo ena anamasulira mawuwa kuti “usandikhudze.” Koma apa sikuti Yesu ankaletsa Mariya Mmagadala kuti asamugwire chifukwa atangoukitsidwa, azimayi ena ‘anagwira mapazi ake’ ndipo sanawaletse. (Mat. 28:9) Zikuoneka kuti Mariya Mmagadala ankaona ngati Yesu akufuna azipita kumwamba. Chifukwa choti ankafunitsitsa kukhalabe ndi Mbuye wakeyo, iye anamugwira mwamphamvu ndipo sankafuna kumusiya. Pofuna kumutsimikizira kuti iye sakupita kumwamba, Yesu anauza Mariya kuti asamukakamire koma apite kukauza ophunzira ake kuti iye waukitsidwa.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 20:28

Mbuyanga ndi Mulungu wanga!: Mawu ake enieni “Ambuye anga ndi Mulungu [ho the·osʹ] wanga!” Akatswiri ena amanena kuti mawu osonyeza kudabwa amenewa ananenedwa kwa Yesu koma kwenikweni ankapita kwa Mulungu, yemwe ndi Atate wake. Pomwe akatswiri ena amaganiza kuti mawu oyambirira achigiriki amasonyeza kuti mawuwa ankapita kwa Yesu. Ngakhale zili choncho, tingamvetse cholinga cha mawu akuti “Mbuyanga ndi Mulungu wanga” ngati titaganizira zimene nkhani yonse imanena. Popeza nkhaniyi ikusonyeza kuti Yesu anali atatumiza uthenga kwa ophunzira ake wonena kuti, “Ine ndikukwera kwa Atate wanga ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanu,” choncho sitinganene kuti Tomasi ankaganiza kuti Yesu ndi Mulungu Wamphamvuyonse. (Onani mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 20:17.) Tomasi anamvapo Yesu akupemphera kwa “Atate” wake n’kumawatchula kuti “Mulungu yekhayo amene ali woona.” (Yoh. 17:1-3) Tomasi ayenera kuti anatchula Yesu kuti “Mulungu wanga” pa zifukwa zotsatirazi: Iye ankaona Yesu monga “mulungu” koma osati Mulungu Wamphamvuyonse. Mwinanso anatchula Yesu mwa njira imeneyi potengera mmene atumiki a Mulungu akale omwe nkhani zawo zinalembedwa m’Malemba Achiheberi ankatchulira angelo amene ankatumidwa ndi Yehova kukapereka uthenga winawake. N’kutheka kuti iye anawerenga nkhani zimene olemba ake kapena anthu a mu nkhanizo ankakambirana ndi angelo ngati kuti akulankhulana ndi Yehova Mulungu. (Yerekezerani ndi Gen. 16:7-11, 13; 18:1-5, 22-33; 32:24-30; Ower. 6:11-15; 13:20-22.) Choncho Tomasi ayenera kuti anatchula Yesu kuti “Mulungu wanga” chifukwa ankazindikira kuti iye anali woimira kapena womulankhulira Mulungu.

Ena amanena kuti kugwiritsa ntchito mawu achigiriki okhala kumbuyo kwa dzina kukusonyeza kuti mawu akuti “mbuye” komanso “mulungu” akunena za Mulungu Wamphamvuyonse. Komabe pa nkhaniyi mawuwa anangogwiritsidwa ntchito potengera kalembedwe ka mawu m’Chigiriki. Zangati zimenezi zimapezekanso m’malemba ena omwe amakhalanso ndi mawu okhala kumbuyo kwa dzina monga pa Luka 12:32 (pomwe amanena za “kagulu ka nkhosa”) komanso pa Akol. 3:18–4:1 (pomwe pali mawu akuti “akazi;” “amuna”; “ana”; “abambo”; “akapolo”; “ambuye”). Zimenezinso ndi zomwe zinachitika pa 1 Pet. 3:7. Choncho kugwiritsa ntchito mawu okhala kumbuyo kwa dzina sikungatithandize kudziwa zomwe Tomasi ankaganiza polankhula mawu amenewa.

NOVEMBER 12-18

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 1-3

“Mpingo Wachikhristu Unalandira Mzimu Woyera”

w86 12/1 29 ¶4-5, 7

Zopereka Zimatithandiza Kukhala Osangalala

Patsiku limene mpingo wachikhristu unayamba mu 33 C.E., anthu 3,000 omwe anali atangobatizidwa kumene “anali kugawana zinthu, kudya chakudya komanso kupemphera.” Kodi zimenezi zinawathandiza bwanji? Zinathandiza kuti chikhulupiriro chawo chipitirizebe kulimba kuti ‘apitirizebe kulabadira zimene atumwi anali kuphunzitsa.’—Mac. 2:41, 42.

Ayuda komanso anthu ena otembenukira kuchiyuda anali atabwera ku Yerusalemu kuti adzangochita chikondwerero cha Pentekosite. Koma amene anabatizidwa n’kukhala Akhristu, ankafuna kuti akhalebe ku Yerusalemuko n’cholinga choti aphunzire zambiri komanso alimbitse chikhulupiriro chawo chatsopanocho. Zimenezi zinachititsa kuti pakhale vuto la chakudya ndi malo ogona. Ena mwa anthuwa analibe ndalama zokwanira pomwe ena anali ndi zochuluka. Choncho anayamba kusonkhanitsa zinthu zofunika kuti athandize amene analibe.—Machitidwe 2:43-47.

Anthu anayamba kugulitsa malo awo komanso kugawana zinthu ndipo ankachita zimenezi mwakufuna kwawo. Palibe amene ankakakamizidwa kugulitsa kapena kupereka zinthu, ndipo zimenezi sikuti zinachititsa kuti anthu ena akhale paumphawi. Sizikutanthauzanso kuti anthu olemera anagulitsa katundu wawo yense n’kusaukiratu. M’malo mwake, chikondi ndi chimene chinalimbikitsa Akhristuwa kuti agulitse zinthu zawo n’kupereka ndalama zonse kuti zithandize kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:12-15.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2 61 ¶1

Yesu Khristu

“Mtumiki Wamkulu wa Moyo.” Monga njira yosonyezera kukoma mtima kwakukulu kwa Atate wake, Yesu anapereka nsembe moyo wake wangwiro. Zimenezi zinathandiza kuti otsatira ena a Khristu akalamulire naye limodzi kumwamba komanso kuti ena adzakhale padziko lapansili n’kumalamulidwa ndi Ufumu wake. (Mat. 6:10; Yoh. 3:16; Aef. 1:7; Aheb. 2:5) Choncho iye anakhala “Mtumiki Wamkulu wa Moyo” kwa anthu onse. (Mac. 3:15) Mawu achigiriki omwe anawagwiritsa ntchito pamenepa amatanthauza “wolamulira wamkulu,” mawu ofanana ndi amene ankatchulira Mose (Mac. 7:27, 35) monga “wolamulira” wa Isiraeli.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

it-1 129 ¶2-3

Mtumwi

Ndi ndani Analowa M’malo mwa Yudasi Isikariyoti Ngati Mtumwi wa Nambala 12?

Chifukwa choti Yudasi anafa atachita zosakhulupirika popereka Yesu, panatsala atumwi 11 okha. Pa masiku 40 omwe Yesu anakhala padzikoli ataukitsidwa mpaka pamene anakwera kumwamba, iye sanasankhe mtumwi wina wolowa m’malo mwa Yudasi. Pa masiku 10 a pakati pa nthawi imene Yesu anakwera kumwamba ndi nthawi ya chikondwerero cha Pentekosite, atumwi anaona kuti pakufunika kusankhidwa munthu wina woti alowe m’malo mwa Yudasi. Iwo sanachite zimenezo kokha chifukwa choti Yudasi anali atamwalira, koma chifukwa cha zoipa zimene anachita monga mmene Malemba omwe Petulo anagwira mawu amanenera. (Mac. 1:15-22; Sal. 69:25; 109:8; yerekezerani ndi Chiv. 3:11.) Koma mtumwi wokhulupirika Yakobo ataphedwa, palibe umboni ulionse wosonyeza kuti atumwi anasankhanso munthu wina kuti amulowe m’malo.—Mac. 12:2.

Malinga ndi zimene Petulo ananena, kuti munthu akhale mtumwi wa Yesu Khristu ankayenera kukhala woti analankhulana naye, kuona ntchito zimene anachita, zozizwitsa zake komanso kuukitsidwa kwake. Poganizira zimenezi, tinganene kuti m’kupita kwa nthawi kusankha munthu wolowa m’malo mwa mtumwi wina kukanakhala kovuta kwambiri, ndipo munthu akanakhala mtumwi pokhapokha ngati waonetsedwa zinthu zimenezi m’masomphenya. Ndiye pa nthawiyo, chikondwerero cha Pentekosite chisanachitike, panapezeka anthu awiri omwe anali oyenerera kulowa m’malo mwa Yudasi. N’kutheka kuti posankha munthu wolowa m’maloyu, atumwi anaganizira lemba la Miyambo 16:33, ndipo anachita mayere n’kusankha Matiya. Kenako “anamuphatikiza pa atumwi 11 aja.” (Mac. 1:23-26) Choncho Matiya ndi m’modzi mwa “atumwi 12” omwe anathetsa nkhani yokhudza ophunzira a Yesu olankhula Chigiriki. (Mac. 6:1, 2) Zikuonekanso kuti Matiya ndi m’modzi mwa “atumwi 12” omwe Paulo anawatchula pamene ankanena za kuonekera kwa Yesu pambuyo poti waukitsidwa pa 1 Akor. 15:4-8. Choncho pamene chikondwero cha Pentekosite chinkachitika, panali atumwi 12 omwe anali ngati maziko a Isiraeli wauzimu.

NOVEMBER 19-25

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 4-5

“Anapitiriza Kulankhula Mawu a Mulungu Molimba Mtima”

it-1 128 ¶3

Mtumwi

Mmene Zinthu Zinalili Mumpingo Wachikhristu. Atumwi analimbikitsidwa kwambiri pamene analandira mzimu wa Mulungu pa Pentekosite. Machaputala 5 oyambirira a buku la Machitidwe a Atumwi amafotokoza mmene atumwi anakhalira olimba mtima polengeza uthenga wabwino komanso polengeza za kuuka kwa Yesu ngakhale kuti ankamenyedwa, kuikidwa m’ndende komanso kuopsezedwa ndi olamulira kuti aphedwa. Patangopita masiku ochepa kuchokera patsiku la Pentekosite, atumwi mothandizidwa ndi mzimu woyera anathandiza kuti mpingo wachikhristu ukule mofulumira kwambiri. (Mac. 2:41; 4:4) Poyamba iwo ankachita utumiki wawo ku Yerusalemu koma kenako anayambanso kulalikira ku Samariya. Ndipo n’kupita kwa nthawi ntchitoyi inafalikira padziko lonse.—Mac. 5:42; 6:7; 8:5-17, 25; 1:8.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1 514 ¶4

Mwala wapakona

Lemba la Salimo 118:22 linaneneratu kuti mwala umene omanga nyumba anaukana, udzakhala “mwala wofunika” (m’Chiheberi, roʼsh pin·nahʹ). Yesu anagwiritsa ntchito mawu a ulosi umenewu ponena za iyeyo kuti ndi amene anali “mwala wapakona wofunika kwambiri” (m’Chigiriki, ke·pha·leʹ go·niʹas). (Mat. 21:42; Maliko 12:10, 11; Luka 20:17) Monga mmene mwala wapakona umakhalira wofunika kwambiri pomanga nyumba, Yesu Khristu ndi mwala wapakona wa mpingo wa Akhristu odzozedwa amene amayerekezeredwa ndi kachisi wauzimu. Nayenso Petulo anagwiritsa ntchito ulosi wa pa Salimo 118:22 ponena za Khristu kuti anali “mwala” umene anthu omanga nyumba anaukana koma womwe unasankhidwa ndi Mulungu kuti ukhale “mwala wofunika kwambiri wapakona.”—Mac. 4:8-12; onaninso 1 Pet. 2:4-7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena