January 28–February 3
MACHITIDWE 27-28
Nyimbo Na. 129 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Paulo Anapita ku Roma”: (10 min.)
Mac. 27:23, 24—Mngelo anauza Paulo kuti iyeyo ndi onse omwe anali m’ngalawamo apulumuka mphepo yamkuntho (bt 208 ¶15)
Mac. 28:1, 2—Ngalawa imene Paulo anakwera inasweka pachilumba cha Melita (bt 209 ¶18-210, ¶21)
Mac. 28:16, 17—Paulo anakafika bwinobwino ku Roma (bt 213 ¶10)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Mac. 27:9—Kodi “nthawi ya kusala kudya kwa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo” imatanthauza chiyani? (“kusala kudya kwa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 27:9, nwtsty)
Mac. 28:11—Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi kutchulidwa kwa chizindikiro chomwe chinali pangalawa yomwe Paulo anakwera? (“Ana . . . a Zeu” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 28:11, nwtsty)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 27:1-12 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. (th phunziro 2)
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 5 min.) lv 139-140 ¶16-17 (th phunziro 3)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Paulo Anayamika Mulungu Ndipo Analimba Mtima”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani mbali ina ya vidiyo yakuti “Chitsulo Chimanola Chitsulo Chinzake.” Limbikitsani onse kuti akaonere vidiyo yonse kunyumba kwawo.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 23 ndi bokosi lakuti “Munthu Wogwidwa ndi Mzimu Woipa”
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 140 ndi Pemphero