MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Lamulo Lovomereza Ntchito Yathu Yolalikira ku Quebec
Pamene Paulo ankaimbidwa mlandu, anapempha kuti akaonekere kwa Kaisara. Nafenso tingatengere chitsanzo chake pa zimene anachita pogwiritsa ntchito ufulu wake monga nzika ya Roma. Onerani vidiyo yakuti Lamulo Lovomereza Ntchito Yathu Yolalikira ku Quebec, kuti muone mmene abale anagwiritsira ntchito malamulo poteteza uthenga wabwino ku Quebec. Kenako yankhani mafunso otsatirawa:
Kodi abale athu ku Quebec anakumana ndi mavuto otani?
Kodi abale anagawira kapepala kapadera kati, nanga zotsatira zake zinali zotani?
Kodi n’chiyani chimene chinachitikira M’bale Aimé Boucher?
Kodi Khoti Lalikulu Kwambiri la ku Canada linaweruza bwanji mlandu wa M’bale Boucher?
Kodi abale anagwiritsa ntchito lamulo lapadera liti, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
Kodi n’chiyani chinachitika apolisi atasokoneza misonkhano yachikhristu molimbikitsidwa ndi wansembe wina?