CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 25-26
Paulo Anapempha Kukaonekera kwa Kaisara Ndipo Kenako Analalikira Mfumu Herode Agiripa
Ngakhale kuti sitikuyenera kumadera nkhawa kuti tikanena chiyani ngati ‘atatitengera kwa abwanamkubwa ndi mafumu,’ tiyenera kukhala “okonzeka nthawi zonse kuyankha” aliyense amene watifunsa za chiyembekezo chimene tili nacho. (Mat. 10:18-20; 1 Pet. 3:15) Kodi tingatengere bwanji chitsanzo cha Paulo ngati anthu otsutsa “akuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo”?—Sal. 94:20.
Timagwiritsa ntchito malamulo amene alipo poteteza uthenga wabwino.—Mac. 25:11
Timachita zinthu mwaulemu tikamalankhula ndi akuluakulu a boma.—Mac. 26:2, 3
Ngati kuli koyenera, timafotokoza mmene uthenga wabwino wathandizira ifeyo komanso anthu ena.—Mac. 26:11-20