CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 23-24
Anaimbidwa Mlandu Wosokoneza Anthu Komanso Kuukira Boma
Ayuda a ku Yerusalemu ‘analumbira mochita kudzitemberera’ kuti aphe Paulo. (Mac. 23:12) Komabe chinali cholinga cha Yehova kuti Paulo apite ku Roma kuti akachitirenso umboni kumeneko. (Mac. 23:11) Mwana wamwamuna wa mlongo wake wa Paulo anadziwa za chiwembuchi ndipo anakamuuza. Zimenezi zinathandiza kuti Paulo asaphedwe. (Mac. 23:16) Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya . . .
zimene anthu ena amachita pofuna kulepheretsa cholinga cha Mulungu?
njira zimene Mulungu angagwiritse ntchito potithandiza?
kulimba mtima?