CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AFILIPI 1-4
“Musamade Nkhawa ndi Kanthu Kalikonse”
Pemphero lingatithandize kuti tisamakhale ndi nkhawa
Tikamapemphera tili ndi chikhulupiriro, Yehova amatipatsa mtendere womwe “umaposa kuganiza mozama kulikonse”
Ngakhale zitakhala kuti palibe zimene tingachite ndi vuto lathulo, Yehova angatithandize kuti tipirire. Angathenso kutithandiza m’njira imene sitimaiganizira.—1 Akor. 10:13