Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 March tsamba 3
  • March 9-15

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • March 9-15
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 March tsamba 3

MARCH 9-15

GENESIS 24

  • Nyimbo Na. 132 ndi Pemphero

  • Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • “Isaki Anapeza Mkazi”: (10 min.)

    • Ge 24:2-4​—Abulahamu anatumiza mtumiki wake kuti akapezere mwana wake mkazi pakati pa anthu otumikira Yehova (wp16.3 14 ¶3)

    • Ge 24:11-15​—Mtumiki wa Abulahamu anakumana ndi Rabeka pachitsime. (wp16.3 14 ¶4)

    • Ge 24:58, 67​—Rabeka anavomera kukwatirana ndi Isaki (wp16.3 14 ¶6-7)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)

    • Ge 24:19, 20​—Kodi zimene Rabeka anachita m’mavesiwa zikutiphunzitsa chiyani? (wp16.3 12-13)

    • Ge 24:65​—N’chifukwa chiyani Rabeka anadziphimba kumutu, nanga tikuphunzirapo chiyani? (wp16.3 15 ¶3)

    • Kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 24:1-21 (th phunziro 2)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: N’chifukwa chiyani tinganene kuti wofalitsayu wagwiritsa ntchito bwino mafunso? Kodi wofalitsayu anayankha zotani atamva zomwe mwininyumba ananena zokhudza Yesu?

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 12)

  • Kuitanira Anthu ku Chikumbutso: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene poitanira anthu ku Chikumbutso. Wofalitsayo asonyeze chidwi. Yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti, Tizikumbukira Imfa ya Yesu kenako kambiranani naye mfundo za m’vidiyoyi. (th phunziro 11)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 25

  • Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba Loweruka pa 14 March: (8 min.) Nkhani yokambirana. Perekani kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kwa aliyense n’kukambirana mfundo zake. Onerani ndi kukambirana vidiyo ya zimene tinganene pogawira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. Fotokozani zimene mpingo wanu wakonza kuti mudzathe kugawira timapepalati kwa anthu onse a m’gawo lanu.

  • “Kodi Ndiitane Ndani?”: (7 min.) Nkhani yokambirana.

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 76

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (Osapitirira 3 min.)

  • Nyimbo Na. 115 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena