MAY 4-10
GENESIS 36-37
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yosefe Anachitiridwa Nsanje”: (10 min.)
Gen. 37:3, 4—Azichimwene ake a Yosefe anayamba kudana naye chifukwa choti bambo ake ankamukonda kwambiri (w14 8/1 12-13)
Gen. 37:5-9, 11—Maloto omwe Yosefe analota anachititsa kuti azichimwene ake azimuchitira nsanje kwambiri (w14 8/1 13 ¶2-4)
Gen. 37:23, 24, 28—Yosefe anachitiridwa zankhanza ndi azichimwene ake chifukwa cha nsanje
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 36:1—N’chifukwa chiyani Esau anapatsidwanso dzina lakuti Edomu? (it-1 678)
Gen. 37:29-32—N’chifukwa chiyani azichimwene ake a Yosefe anakaonetsa Yakobo mkanjo wa Yosefe uli ndi magazi? (it-1 561-562)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 36:1-19 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kulankhula Zomveka, kenako kambiranani phunziro 17 m’kabuku ka Kuphunzitsa.
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) w02 10/15 30-31—Mutu: N’chifukwa Chiyani Akhristu Ayenera Kukhala ndi Nsanje Yofanana ndi ya Mulungu? (th phunziro 6)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Mwakonzekera?”: (15 min.) Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mkulu. Onerani vidiyo yakuti Zimene Tingachite Pokonzekera Masoka Achilengedwe. Tchulaninso zilengezo zochokera ku ofesi ya nthambi kapena ku bungwe la akulu ngati zilipo.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 83
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 108 ndi Pemphero