MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Zinthu za M’chilengedwe Zimatiphunzitsa Chiyani pa Nkhani ya Kulimba Mtima?
Yehova amatiphunzitsa mmene tingakhalire ndi makhalidwe omwe iye ali nawo kudzera mwa amuna ndi akazi otchulidwa m’Baibulo. Njira inanso imene amatiphunzitsira makhalidwewa ndi kudzera m’zinthu zimene analenga. (Yob 12:7, 8) Kodi tingaphunzire chiyani kwa mkango, hatchi, msulu, choso ndiponso njovu pa nkhani ya kulimba mtima?
ONERANI VIDIYO YAKUTI PHUNZIRANI KULIMBA MTIMA KUCHOKERA KU ZINTHU ZA M’CHILENGEDWE, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi mikango yaikazi imasonyeza bwanji kulimba mtima ikamateteza ana ake?
Kodi mahatchi amaphunzitsidwa bwanji kuti azikhala olimba mtima akapita ku nkhondo?
N’chifukwa chiyani msulu suopa njoka za poizoni?
Kodi timbalame totchedwa choso timasonyeza bwanji kulimba mtima?
Kodi njovu zimateteza bwanji zinzawo molimba mtima?
Kodi nyamazi zikukuphunzitsani chiyani pa nkhani ya kulimba mtima?