August 10-16
EKISODO 15-16
Nyimbo Na. 149 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Tamandani Yehova Poimba Nyimbo”: (10 min.)
Eks 15:1, 2—Mose ndi amuna a Chiisiraeli anaimba nyimbo zotamanda Yehova (w95 10/15 11 ¶11)
Eks 15:11, 18—Yehova ndi woyenera kutamandidwa (w95 10/15 11-12 ¶15-16)
Eks 15:20, 21—Miriamu ndi akazi a Chiisiraeli anaimba nyimbo zotamanda Yehova (it-2 454 ¶1; 698)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks 16:13—Pamene Aisiraeli anali m’chipululu, kodi n’kutheka kuti Yehova anasankha kuwapatsa zinziri pa zifukwa ziti? (w11 9/1 14)
Eks 16:32-34—Kodi mtsuko wa mana unkasungidwa kuti? (w06 1/15 31)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 16:1-18 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi a Linda anagwiritsa ntchito bwanji mafunso mwaluso? Kodi anafotokoza bwanji Malemba momveka bwino?
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako mugawireni buku kapena kabuku kopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 3)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 5 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako musonyezeni ndi kukambirana naye mfundo za m’vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? (koma musaonetse vidiyoyi). (th phunziro 9)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzitamanda Yehova Pochita Upainiya”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Alongo Atatu Apachibale a ku Mongolia. Kenako funsani m’bale kapena mlongo amene akutumikira monga mpainiya kapena amene anatumikirapo m’mbuyomu mafunso otsatirawa: Kodi mwakumanapo ndi mavuto otani? Ndi madalitso ati amene mwapeza?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 95
Mawu Omaliza (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 131 ndi Pemphero