September 28–October 4
EKISODO 29-30
Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Chopereka kwa Yehova”: (10 min.)
Eks 30:11, 12—Yehova anauza Mose kuti achite kalembera (it-2 764-765)
Eks 30:13-15—Munthu aliyense amene anawerengedwa anapereka chopereka kwa Yehova (it-1 502)
Eks 30:16—Choperekacho chinkagwiritsidwa ntchito “pa utumiki wa pachihema chokumanako” (w11 11/1 12 ¶1-2)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Eks 29:10—Kodi zinkatanthauza chiyani pamene ansembe ‘ankaika manja awo pamutu wa ng’ombe’? (it-1 1029 ¶4)
Eks 30:31-33—N’chifukwa chiyani linali tchimo lalikulu munthu akapanga mafuta ogwiritsidwa ntchito pa kudzoza kopatulika n’kupaka munthu wamba? (it-1 114 ¶1)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Eks 29:31-46 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba posonyeza mmene mungalalikire mukakhala pa kamera kapena pogwiritsa ntchito intakomu. (Ngati m’gawo lanu mulibe makamera kapena maintakomu, sonyezani zimene mungachite polalikira munthu amene akulankhula nanu ali m’nyumba koma sanatsegule chitseko.) (th phunziro 2)
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 5 min.) bhs 113 ¶18 (th phunziro 13)
Nkhani: (Osapitirira 5 min.) km 1/11 4 ¶5-7; 6, bokosi—Mutu: Zinthu Zina Zimene Mungachite pa Kulambira kwa Pabanja. (th phunziro 20)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Mungapereke Nthawi ndi Mphamvu Zanu?” (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani mbali ina ya vidiyo yakuti Pakukonzedwa Zomanga Beteli Yatsopano.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (Osapitirira 30 min.) jy mutu 102
Mawu Omaliza (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 15 ndi Pemphero