Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mphatso Yothandiza kwa Mabanja
    Utumiki wa Ufumu—2011 | January
    • 5. Kodi nthawi yonse ya Kulambira kwa Pabanja izingothera pokambirana monga banja? Fotokozani.

      5 Kodi Nthawi Yonse ya Kulambira kwa Pabanja Izingothera Pokambirana Monga Banja? Anthu okwatirana komanso mabanja amene ali ndi ana amalimbikitsana akamakambirana nkhani za m’Malemba. (Aroma 1:12) Onse m’banjamo amayamba kukondana. Choncho, kukambirana mfundo za m’malemba ndi kofunika kwambiri pa Kulambira kwa Pabanja. Komabe, aliyense m’banjamo akhoza kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi pophunzira Baibulo payekha. Mwachitsanzo, pambuyo poti amaliza kukambirana monga banja, onse akhoza kukhalabe pamodzi koma aliyense akupitiriza kuphunzira payekha, mwina angamapitirize kukonzekera misonkhano kapena kuwerenga magazini. Mabanja ena amasankha kusayatsa TV chigawo chonse cha tsiku chimene amachita Kulambira kwa Pabanja.

      6. Kodi zokambiranazo zizichitika motani?

      6 Kodi Zokambiranazo Zizichitika Motani? Sikuti nthawi zonse kukambiranako kuzikhala kwa mafunso ndi mayankho. Mabanja ambiri amakhala ndi ndondomeko yofanana ndi imene timakhala nayo kumisonkhano kuti Kulambira kwa Pabanja kwawo kuzikhala kosangalatsa komanso kochititsa chidwi. Amagawa zokambiranazo m’mbali zosiyanasiyana komanso amaziphunzira m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, angawerenge Baibulo pamodzi, kukonzekera misonkhano ina ndi kuyerekeza zimene angakachite mu utumiki. Tsamba 6 lili ndi zina zimene mungachite.

      7. Kodi makolo ayenera kuyesetsa kuti zokambiranazo zizikhala zotani?

      7 Kodi Makolo Ayenera Kukhala ndi Cholinga Choti Mzimu wa Zokambiranazo Uzikhala Wotani? Banja lanu likhoza kumaphunzira bwino ngati phunzirolo likuchitika mwachikondi komanso m’njira yokhala ngati mukucheza. Nthawi zina mukhoza kuchitira phunziro lanu panja ngati nyengo ili bwino. Mukhoza kumakhala ndi kanthawi kopuma kaye pang’ono ngati pakufunikira kutero. Mabanja ena amakonza zokhala ndi zosangalatsa zina akamaliza phunzirolo. Makolo ayenera kupewa kugwiritsa ntchito mpata umenewu kudzudzula kapena kupereka chilango kwa ana. Komabe, ngati adziwa zoti pabanjapo pali chizolowezi kapena vuto linalake, akhoza kugwiritsa ntchito nthawi ina ya phunzirolo kuti akambirane njira yothetsera vutolo. Ngakhale zili choncho, ngati pali nkhani ina yachinsinsi yokhudza mwana wina, ndi bwino kukambirana naye payekha nthawi ina mkati mwa mlunguwo kuti musamuchititse manyazi pamaso pa abale ake. Kulambira kwa Pabanja sikuyenera kukhala kosasangalatsa kapena kotopetsa, koma kuyenera kusonyeza kuti Mulungu amene timamulambira ndi wachimwemwe.—1 Tim. 1:11.

  • Ndandanda ya Mlungu wa January 31
    Utumiki wa Ufumu—2011 | January
    • Ndandanda ya Mlungu wa January 31

      MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 31

      Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero

      □ Phunziro la Baibulo la Mpingo:

      cf mutu 2 ndime 1-8 (Mph. 25)

      □ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:

      Kuwerenga Baibulo: Nehemiya 1-4 (Mph. 10)

      Na. 1: Nehemiya 2:11-20 (Osapitirira mph. 4)

      Na. 2: Kodi Lemba la Yohane 1:1 Limatsimikizira Kuti Yesu ndi Mulungu?—rs tsa. 426 ndime 4 mpaka tsa. 427 ndime 1 (Mph. 5)

      Na. 3: Zimene Tingachite Potsatira Mawu a Yesu a pa Mateyu 22:21 (Mph. 5)

      □ Msonkhano wa Utumiki:

      Nyimbo Na. 52

      Mph. 5: Zilengezo.

      Mph. 20: “Mphatso Yothandiza Kwa Mabanja.”—Gawo 2. (Ndime 7-13) Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kufotokoza mmene mabanja awo apindulira pogwiritsa ntchito mfundo zina zomwe zili pa tsamba 6.

      Mph. 10: “Phunzitsani Ana Anu Kuti Adzakhale Atumiki.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze njira zimene makolo awo anawathandizira kuti akhale ndi zolinga mu utumiki komanso kuyesetsa kuzikwaniritsa.

      Nyimbo Na. 41 ndi Pemphero

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena