Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
DECEMBER 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 10-11
“Tizikonda Yehova Kuposa Mmene Timakondera Achibale Athu”
it-1 1174
Zosaloledwa
Moto Ndiponso Zofukiza Zosaloledwa. Palemba la Levitiko 10:1, mawu a Chiheberi akuti zar (kapena kuti, za·rahʹ; otanthauza kuti, zachilendo) anagwiritsidwa ntchito ponena za ‘moto wosaloledwa ndi Yehova’ umene ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu, anapereka kwa iye ngakhale kuti “sanawalamule.” Choncho iwo anaphedwa ndi moto. (Le 10:2; Nu 3:4; 26:61) Kenako Yehova anauza Aroni kuti: “Pamene mukubwera kuchihema chokumanako, iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena zakumwa zina zoledzeretsa, kuti mungafe. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale, kuti muzisiyanitsa pakati pa chinthu chopatulika ndi choipitsidwa ndiponso pakati pa chodetsedwa ndi choyera. Kutinso muziphunzitsa ana a Isiraeli malamulo onse amene Yehova wanena kwa iwo kudzera mwa Mose.” (Le 10:8-11) Zimenezi zikusonyeza kuti Nadabu ndi Abihu ayenera kuti anali ataledzera ndipo izi n’zimene zinachititsa kuti apereke moto umene Mulungu sanawalamule. Motowo uyenera kuti unali wosaloledwa chifukwa cha nthawi imene anauperekera, malo kapena mmene anauperekera. Apo ayi, unali wosayenera chifukwa choti zofukiza zake zinali zopangidwa ndi msanganizo wosiyana ndi umene unafotokozedwa pa Ekisodo 30:34, 35. Koma kuledzera kwawo sikunali chifukwa chomveka choti asalangidwe.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 111 ¶5
Zinyama
Anthu amene ankatsatira Chilamulo cha Mose okha ndi amene ankayenera kupewa nyama zimene zinaletsedwa m’Chilamulochi. Paja lemba la Levitiko 11:8 limanena za nyama zimenezi kuti: “Zikhale zodetsedwa kwa inu,” kutanthauza kwa Aisiraeli. Popeza Chilamulochi chinasiya kugwira ntchito pamene Yesu Khristu anapereka moyo wake nsembe, malamulo oletsa kudya nyama zina anachotsedwa ndipo anthu onse anayamba kumangotsatira zimene Mulungu anauza Nowa pambuyo pa Chigumula.—Akl 2:13-17; Ge 9:3, 4.
DECEMBER 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 12-13
“Zimene Tingaphunzire pa Malamulo Okhudza Khate”
it-2 238 ¶3
Khate
Pazovala ndi m’nyumba. Khate linkatuluka pansalu ya ubweya wa nkhosa, nsalu zina komanso pachikopa. Nthawi zina khatelo linkatha kuchoka chinthucho chikachapidwa ndipo ankachiikanso pachokha kuti khatelo lisafalikire. Koma ngati nthendayo inapitiriza kuoneka yobiriwira mopitira ku chikasu kapena yofiirira pa chinthucho, ndiye kuti inali khate loopsa ndipo chinthucho chinkafunika kuotchedwa. (Le 13:47-59) Ngati mbali ina ya khoma la nyumba inkaoneka yobiriwira mopitira ku chikasu kapena yofiira, wansembe ankalamula kuti atulutse chilichonse m’nyumbayo n’kuitseka. Mwina ankafunika kuchotsa miyala yokhala ndi khatelo komanso kupala mkati mwa nyumbayo kenako n’kukataya zinthuzo kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. Nthendayo ikayambiranso, wansembe ankanena kuti nyumbayo ndi yodetsedwa ndipo inkagwetsedwa. Kenako zinthu za panyumbayo zinkakatayidwa kumalo odetsedwa. Koma wansembe akanena kuti nyumbayo ndi yoyera, pankakhala mwambo woyeretsa nyumbayo. (Le 14:33-57) Anthu ena amanena kuti khate limene linkakhala pazovala kapena m’nyumba linkakhala mtundu wina wa nkhungu, koma palibe umboni wotsimikizira zimenezi.
DECEMBER 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 14-15
“Timafunika Kukhala Oyera Kuti Tizilambira Mulungu Movomerezeka”
it-1 263
Kusamba
Aisiraeli ankafunika kuchita mwambo wosamba pa zifukwa zosiyanasiyana. Munthu aliyense amene anachira khate lake, aliyense amene anakhudza zinthu zimene zinagwiridwa ndi anthu amene ‘akukha,’ mwamuna aliyense amene anatulutsa umuna, mkazi aliyense amene wamaliza masiku ake osamba, mkazi amene amakha magazi pa zifukwa zina koma wangosiya kumene kapenanso aliyense amene wagonana ndi munthu ankakhala “wodetsedwa” ndipo ankafunika kusamba. (Le 14:8, 9; 15:4-27) Munthu akakhala mumsasa limodzi ndi mtembo kapena kuukhudza ankakhala “wodetsedwa” ndipo ankafunika kudziyeretsa ndi madzi. Ngati munthu sanatsatire malamulowa, ‘ankaphedwa kuti asakhalenso pakati pa mpingowo, chifukwa waipitsa malo opatulika a Yehova.’ (Nu 19:20) Choncho n’zomveka kuti kusamba kumaimira kukhala oyera pamaso pa Yehova. (Sl 26:6; 73:13; Yes 1:16; Eze 16:9) Kusamba pogwiritsa ntchito mawu achoonadi a Yehova, omwe ali ngati madzi, kungatithandize kukhala oyera.—Aef 5:26.
it-2 372 ¶2
Kusamba kwa Mkazi
Mkazi ankaonedwa kuti ndi wodetsedwa akakha magazi pa nthawi yomwe si yosamba kapena “akapitiriza kukha magazi nthawi yake yokhala wodetsedwa chifukwa cha kusamba kwake itatha.” Pa nthawiyi, chilichonse chimene ankagonera kapena kukhalira chinkakhala chodetsedwa komanso munthu aliyense wokhudza chinthucho ankakhala wodetsedwa. Akasiya kukha magazi pa nthawi imene si yosamba ankafunika kudikira masiku 7 kuti akhale woyera. Pa tsiku la 8, mkaziyo ankapita ndi nkhunda ziwiri kapena njiwa ziwiri kwa wansembe yemwe ankapereka imodzi kwa Yehova monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza.—Le 15:19-30.
it-1 1133
Malo Oyera
2. Chihema chokumanako ndipo kenako kachisi. Malo onse, kuphatikizapo bwalo la chihema komanso mabwalo a kachisi anali malo oyera. (Eks 38:24; 2Mb 29:5; Mac 21:28) Zinthu zofunika kwambiri zomwe zinali m’bwaloli zinali guwa la nsembe komanso beseni lamkuwa. Zinthuzi zinali zoyera. Anthu amene ankaloledwa kulowa m’bwalo la chihema ndi okhawo amene anali atadziyeretsa ndipo anthu odetsedwa sankaloledwa kulowa m’mabwalo a kachisi. Mwachitsanzo, mkazi amene anali wodetsedwa sankayenera kukhudza chinthu chilichonse choyera kapena kulowa m’malo oyera. (Le 12:2-4) Zikuoneka kuti Aisiraeli akapitiriza kuchita zinthu zodetsa ankaonedwa kuti akuipitsanso chihema. (Le 15:31) Anthu amene ankabweretsa nsembe zowayeretsa ku khate ankazisiya pageti la bwalo la chihema. (Le 14:11) Munthu wodetsedwa akadya nsembe yachiyanjano kuchihema kapena kukachisi ankaphedwa.—Le 7:20, 21.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 665 ¶5
Khutu
Pa mwambo wolonga unsembe ku Isiraeli, Mose anauzidwa kuti atenge magazi a nkhosa yamphongo n’kuwaika pakhutu lakumanja la Aroni ndi ana ake aamuna komanso padzanja ndi phazi lakumanja. Izi zinkasonyeza kuti zimene iwo ankamvetsera, ntchito imene ankagwira komanso zimene ankachita pa moyo wawo zinkayenera kukhudzidwa ndi udindo wawo wokhala ansembe. (Le 8:22-24) Mofanana ndi zimenezi, wakhate akayeretsedwa, Chilamulo chinkanena kuti wansembe ayenera kuika pakhutu lake lakumanja magazi a nkhosa yamphongo komanso mafuta amene aperekedwa nsembe ya kupalamula. (Le 14:14, 17, 25, 28) Zofanana ndi zimenezi zinkachitikanso kapolo akasankha kuti apitirize kutumikira mbuye wake kwa moyo wake wonse. Mbuye wakeyo ankayenera kupita naye pafelemu ya chitseko n’kumuboola khutu ndi choboolera. Zikuoneka kuti kuchita zimenezi kunkasonyeza kuti kapoloyo ankafuna kupitiriza kumvera mbuye wake.—Eks 21:5, 6.
DECEMBER 28–JANUARY 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 16-17
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 226 ¶3
Azazeli
Mogwirizana ndi zimene ananena mtumwi Paulo, pamene Yesu anapereka moyo wake wangwiro nsembe chifukwa cha machimo a anthu, anachita zazikulu kuposa zimene “magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi” ankachita. (Ahe 10:4, 11, 12) Yesu anakhala ngati ‘mbuzi ya Azazeli’ chifukwa “anatinyamulira matenda athu” komanso “anabayidwa chifukwa cha zolakwa zathu.” (Yes 53:4, 5; Mt 8:17; 1Pe 2:24) Yesu ‘ananyamula’ machimo a anthu onse amene amasonyeza kuti amakhulupirira nsembe yake. Zimene anachitazi zikusonyeza zomwe Mulungu wakonza zoti athetseretu uchimo. Choncho mwa njira zimenezi, mbuzi “ya Azazeli” imaimira nsembe ya Yesu Khristu.