Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsamba 9
  • Timathokoza Mulungu ndi Khristu Chifukwa cha Ufulu Womwe Tidzakhale Nawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Timathokoza Mulungu ndi Khristu Chifukwa cha Ufulu Womwe Tidzakhale Nawo
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amatithandiza Tikamakumana ndi Mayesero
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Kodi Mayesero Tiziwaona Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Tikakumana ndi Mayesero
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 January tsamba 9
Yesu ali kumwamba pampando wachifumu, akuyang’ana padziko lapansi ndipo kuwala kwa mpando wachifumu wa Yehova kukuonekera kumbuyo kwake.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Timathokoza Mulungu ndi Khristu Chifukwa cha Ufulu Womwe Tidzakhale Nawo

Kodi mukulimbana ndi mavuto ati pa moyo wanu? Kodi ndinu mutu wabanja ndipo muli ndi maudindo ambiri? Kodi ndinu kholo koma mulibe mwamuna kapena mkazi ndipo mumafunika kusamalira banja lanu? Kodi ndinu wachinyamata amene amapita kusukulu ndipo mumavutitsidwa ndi anzanu a kusukuluko? Kapena kodi mukulimbana ndi matenda kapenanso mavuto obwera chifukwa cha ukalamba? Aliyense akukumana ndi mavuto. Akhristu ambiri akukumana ndi mavuto angapo nthawi imodzi. Komabe tikudziwa kuti posachedwapa Yehova adzathetsa mavuto onsewa.​—2Ak 4:​16-18.

Panopa timalimbikitsidwa kudziwa kuti Yehova amamvetsa mavuto athu, amayamikira kukhulupirika ndi kupirira kwathu komanso kuti watisungira madalitso osaneneka. (Yer 29:​11, 12) Nayenso Yesu amachita chidwi ndi zimene zikutichitikira. Iye amatitsimikizira kuti ‘ali nafe pamodzi’ pamene tikugwira ntchito imene anatisiyira. (Mt 28:20) Tikamaganizira za ufulu umene tidzakhale nawo mu Ufumu wa Mulungu, chikhulupiriro chathu chimalimba komanso timakhala okonzeka kupirira mavuto omwe tikukumana nawo.​—Aro 8:​19-21.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, PITIRIZANI KUYANG’ANITSITSA YESU PAMENE MPHEPO YAMKUNTHO IKUBWERA​—MADALITSO AMENE UFUMU UDZABWERETSE NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi anthu anakhala bwanji otalikirana ndi Mulungu, ndipo zotsatira zake ndi zotani?

  • Kodi anthu omwe ndi okhulupirika kwa Yehova akuyembekezera zotani m’tsogolo?

  • N’chiyani chikuthandiza kuti zimene akuyembekezerazo zidzatheke?

  • Kodi ndi madalitso ati a m’dziko latsopano amene inuyo mukuyembekezera mwachidwi?

Anthu akusangalala chifukwa cha madalitso amene apeza m’Paradaiso. 1. Mlongo akukumbatira munthu yemwe waukitsidwa. 2. Anthu akusangalala chifukwa ali ndi chakudya chokwanira, dziko lokongola komanso ali pa mtendere.

Muziyerekezera muli m’dziko latsopano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena