MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Amatithandiza Tikamakumana ndi Mayesero
M’masiku otsiriza ano, tikukumana ndi mayesero osiyanasiyana. Nthawi zina, timaona kuti mayesero ena amakhala ovuta kwambiri kuwapirira. Komabe ngati titapitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, iye akhoza kutithandiza kupirira ngakhale mayesero ovuta kwambiriwo. (Yes 43:2, 4) Ndiye kodi tingatani kuti tikhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova pamene tikukumana ndi mayesero?
Pemphero. Tikamuuza Yehova zamumtima mwathu, iye amatipatsa mtendere komanso mphamvu kuti tipirire.—Afi 4:6, 7; 1At 5:17.
Misonkhano. Kuposa kale lonse, panopa tikufunika chakudya chauzimu chimene Yehova amatipatsa komanso kusonkhana limodzi ndi abale athu. (Ahe 10:24, 25) Tikamakonzekera, kupezeka komanso kuyankha pa misonkhano, mzimu wa Yehova umatithandiza kwambiri.—Chv 2:29.
Kulalikira. Zimakhala zosavuta kuganizira zinthu zabwino ngati timachita zonse zomwe tingathe kuti tizichita zambiri mu utumiki. Timalimbitsanso ubwenzi wathu ndi Yehova komanso Akhristu anzathu.—1Ak 3:5-10.
ONERANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA ADZAKHALA NAWE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OSATIRAWA:
Kodi n’chiyani chinathandiza Malu kuti akhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova pamene ankakumana ndi mayesero?
Mofanana ndi Malu, kodi mawu opezeka pa Salimo 34:18 angatilimbikitse bwanji pamene tikukumana ndi mayesero?
Kodi zomwe zinachitikira Malu zikusonyeza bwanji kuti Yehova amatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” tikamakumana ndi mayesero?—2Ak 4:7.