MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Amatisonyeza Chikondi Chokhulupirika
Yehova amakuonani kuti ndinu wamtengo wapatali. (Yes 43:4) Anafuna kuti mukhale mnzake ndipo anakubweretsani m’gulu lake. Chifukwa chakuti munadzipereka komanso kubatizidwa, ndinu a Yehova. Iye adzakusamalirani monga chuma chake chapadera, ngakhale pamene zinthu zavuta, ndipo adzakusonyezani chikondi chokhulupirika kudzera m’gulu lake.—Sl 25:10
Tingasonyeze kuyamikira kwambiri chikondi chokhulupirika cha Yehova, tikaona mmene gulu lake lathandizira anthu pa nthawi ya ngozi zam’chilengedwe zimene zachitika posachedwapa.
ONERANI VIDIYO YAKUTI LIPOTI LA KOMITI YA OGWIRIZANITSA LA 2019, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi Komiti ya Ogwirizanitsa inakonzekeretsa bwanji maofesi a nthambi padziko lonse za mmene angakonzekerere ngozi zosiyanasiyana?
Kodi gulu la Yehova linapereka bwanji malangizo komanso thandizo ku Indonesia ndi ku Nigeria?
Kodi n’chiyani chakusangalatsani ndi mmene gulu lachitira zinthu pa nthawi ya mliri wa COVID-19?