September 26–October 2
1 MAFUMU 15-16
Nyimbo Na. 73 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Mumachita Zinthu Molimba Mtima Ngati Asa?”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
1Mf 16:34—Kodi lembali lalimbitsa bwanji chikhulupiriro chanu kuti malonjezo onse a Yehova adzakwaniritsidwa? (w98 9/15 21-22)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) 1Mf 15:25–16:7 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene pa ntchito yapadera yoyambitsa maphunziro a Baibulo. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 12)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha zimene tinganene pa ntchito yapadera yoyambitsa maphunziro a Baibulo. Yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? (th phunziro 16)
Phunziro la Baibulo: (5 min.) lff phunziro 07 mfundo 6 (th phunziro 6)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Asilikali Olimba Mtima a Khristu: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani funso ili, Kodi mukuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Benjamin ndi Sruthi?
Zimene Gulu Lathu Lachita: (10 min.) Onerani vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya September.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lff phunziro 20
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero