Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 September tsamba 7
  • Muzidalira Yehova Mukakumana ndi Mavuto Azachuma

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzidalira Yehova Mukakumana ndi Mavuto Azachuma
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amaona Kuti Ndinu Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Pitirizani Kudikira Mopirira
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu Chidzakhala Cholimba?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Habakuku
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 September tsamba 7
Zithunzi za muvidiyo yakuti “Mangani Nyumba Yolimba​—‘Muzikhala Okhutira Ndi Zimene Muli Nazo.’” 1. Ángel akuwerenga Baibulo. 2. Lester ndi mkazi wake akuwerenga Baibulo limodzi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzidalira Yehova Mukakumana ndi Mavuto Azachuma

Moyo m’masiku otsirizawa wangodzaza ndi mavuto. Pamene tikuyandikira mapeto a dzikoli, mavuto aziwonjezereka kwambiri ndipo nthawi zina tikhoza kumasowa zinthu zofunika pa moyo. (Hab 3:16-18) Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira tikakumana ndi mavuto azachuma? Tiyenera kupitiriza kudalira Yehova Mulungu wathu. Iye analonjeza kuti adzasamalira atumiki ake ndipo adzawapatsa zonse zimene amafunikira zivute zitani.​—Sl 37:18, 19; Ahe 13:5, 6.

Zimene mungachite:

  • Muzipempha Yehova kuti akutsogolereni, akupatseni nzeru komanso akuthandizeni.​—Sl 62:8

  • Muzikhala okonzeka kugwira ntchito iliyonse ngakhale imene simunagwirepo.​—g 1/10 8-9, mabokosi

  • Muzichita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse, kuphatikizapo kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse, kupezeka pa misonkhano ya mpingo komanso kugwira nawo ntchito yolalikira

ONERANI VIDIYO YAKUTI MANGANI NYUMBA YOLIMBA​—‘MUZIKHALA OKHUTIRA NDI ZIMENE MULI NAZO,’ KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi mavuto ati amene mabanja ena anakumana nawo?

  • Kodi chinthu chofunika kwambiri pa moyo n’chiyani?

  • Kodi tingathandize bwanji anthu amene akukumana ndi mavuto azachuma?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena