September 18-24
ESITERE 6-8
Nyimbo Na. 115 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Zimene Tikuphunzira pa Nkhani ya Kulankhulana Bwino”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Est 7:4—Kodi kuwonongedwa kwa Ayuda kukanawonongetsa bwanji ‘zinthu zambiri za mfumu’? (w06 3/1 11 ¶1)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Est 8:9-17 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 3)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo wobwereza. Yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti, Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?, kenako kambiranani naye mfundo za muvidiyoyi. (th phunziro 12)
Nkhani: (5 min.) w22.01 10-11 ¶8-10—Mutu: Tiziphunzitsa Mogwira Mtima Ngati Yakobo—Uthenga Wathu Uzikhala Wosavuta Kumva. (th phunziro 17)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani”: (15 min.) Nkhani yokambirana komanso vidiyo.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lff phunziro 58
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 124 ndi Pemphero