November 20-26
YOBU 18-19
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musamasiye Akhristu Anzanu”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Yob 19:1, 2—Kodi tikuphunzira chiyani pa mmene Yobu anayankhira anzake omwe anamulankhula mawu opweteka? (w94 10/1 32)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Yobu 18:1-21 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 12)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo wobwereza. Muitanireni kumisonkhano yathu ndipo yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?, kenako kambiranani naye mfundo za muvidiyoyi. (th phunziro 3)
Nkhani: (5 min.) w20.10 17 ¶10-11—Mutu: Muzilimbikitsa Ophunzira Baibulo Kuti Apeze Anzawo Mumpingo. (th phunziro 20)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Khalani Bwenzi la Yehova—Uzithandiza Ena: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako ngati n’zotheka funsani ana omwe munawasankhiratu mafunso awa: Kodi ana angathandize bwanji anthu ena?
Kodi ungakonde kuchita chiyani kuti uthandize ena?
“Kulimbikitsa Anthu Omwe Amatumikira pa Beteli”: (10 min.) Nkhani yokambirana komanso vidiyo.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) bt mutu 2 ¶8-15
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 63 ndi Pemphero