Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb24 January tsamba 6-7
  • January 22-28

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • January 22-28
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2024
mwb24 January tsamba 6-7

JANUARY 22-28

YOBU 38-39

Nyimbo Na. 11 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kodi Mumapeza Nthawi Yoona Chilengedwe?

(10 min.)

Atalenga dzikoli, Yehova anapeza nthawi yoti aone zomwe analengazo (Ge 1:10, 12; Yob 38:5, 6; w21.08 10 ¶7)

Angelo anapeza nthawi yoti aone chilengedwe cha Yehova (Yob 38:7; w20.08 14 ¶2)

Tingamadalire kwambiri Yehova ngati timapeza nthawi yoona ndi kuyamikira zimene iye analenga (Yob 38:32-35; w23.03 17 ¶8)

Mayi ndi mwana wake akuonerera gulugufe akuuluka panja pa nyumba yawo.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Yob 38:8-10—Kodi mavesiwa akutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova monga Wopereka Malamulo? (it-2 222)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Yob 39:1-22 (th phunziro 5)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Sonyezani mmene mwaulemu mungasiyire kukambirana ndi munthu amene akuoneka kuti sakufuna kulankhula nanu. (lmd phunziro 2 mfundo 3)

5. Ulendo Wobwereza

(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pa ulendo wapita, mwininyumbayo anakuuzani kuti wachibale wake kapena mnzake wamwalira. (lmd phunziro 9 mfundo 3)

6. Nkhani

(5 min.) lmd zakumapeto A mfundo 1—Mutu: Zinthu Zomwe Zikuchitika Masiku Ano Zikusonyeza Kuti Posachedwapa Zinthu Zisintha. (th phunziro 16)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 111

7. Kuchita Chidwi ndi Chilengedwe Kumatithandiza Kuti Tiziganizira Zinthu Zofunika Kwambiri

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yobu akuganizira za nyama zochititsa chidwi zomwe Mulungu analenga monga mvuu, dokowe, nthiwatiwa, ng’ona, chiwombankhanga, hatchi komanso ng’ombe yamphongo yam’tchire. Kukuwomba mphepo yamphamvu ndipo Elihu limodzi ndi anzake atatu a Yobu omwe ankanamizira kudzamutonthoza, akhala naye chapafupi.

Pa nthawi imene Yobu ankatsutsidwa ndi anzake atatu komanso Satana, iye ankangoganizira za mavuto ake komanso zinthu zopanda chilungamo zomwe zinkamuchitikira.

Werengani Yobu 37:14. Kenako funsani funso lotsatirali:

Kodi Yobu ankafunika kuchita chiyani kuti ayambenso kuona zinthu moyenera?

Tikapanikizika ndi mavuto, kuchita chidwi ndi chilengedwe kungatithandize kuti tizikumbukira kuti Yehova ndi wamkulu, kungatilimbikitse kuti tikhalebe okhulupirira komanso kungatithandize kuti tizimudalira kwambiri kuti atisamalira.—Mt 6:26.

Onerani VIDIYO yakuti Zimene Tikuphunzira M’buku la Yobu—Zimene Zinyama Zimatiphunzitsa. Kenako funsani funso lotsatirali:

Kodi vidiyoyi yakulimbikitsani bwanji kuti muzidalira kwambiri Yehova?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 4 ¶13-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 54 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena